Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Ofalitsa angagawire kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 timene ali nato monga: Dikirani!, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba mukagawira bukuli. Sonyezani mwininyumba phindu la bukuli popanga naye phunziro la Baibulo mwachidule. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Ngati mwininyumba ali kale ndi kapepala kameneka yesetsani kuyamba naye phunziro la Baibulo.
◼ Mlungu wa msonkhano wachigawo, msonkhano wadera ndi tsiku la msonkhano wapadera mipingo siyenera kuchita Phunziro la Baibulo la Mpingo, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ndi Msonkhano wa Utumiki. Chifukwa cha zimenezi, tikukulimbikitsani nonse kuwerenga nkhani za misonkhano itatu imeneyi kunyumba monga pa Kulambira kwa Pabanja.