Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Magazini athu amakhala ndi uthenga wopulumutsa moyo. Choncho n’zolimbikitsa kuona kuti anthu ambiri akuwerenga magaziniwa. Mwachitsanzo, m’mwezi wa December 2010, tinagawira anthu magazini okwanira 408,865. Komanso tinachititsa maphunziro a Baibulo 82,720. Izi zikutanthauza kuti wofalitsa aliyense anali ndi phunziro la Baibulo. Mwezi umenewu ndi umene tinachititsa maphunziro a Baibulo ambiri kuposa mwezi wina uliwonse m’chaka chonsecho. Tikukhulupirira kuti ambiri mwa anthu amenewa apindula ndi madzi a moyo amene akuwalandirawa. (Chiv. 22:17) Komanso tinasangalala titalandira malipoti ambiri a miyezi yam’mbuyo. Tikukhulupirira kuti mabungwe a akulu apitiriza kuonetsetsa kuti akutumiza malipoti autumiki wakumunda ku ofesi ya nthambi mwezi uliwonse.