Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, agawireni kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Gawirani kabuku kakuti, Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati pakhomopo pali ana, mungagawire buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso kapena Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli ndipo sakufuna phunziro la Baibulo, ofalitsa angamupatse magazini ena alionse akale kapena kabuku kamene mwininyumbayo angakonde.