Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Lemba la Yesaya 60:22 limati: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Monga mbali ya kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu, m’chaka cha utumiki chapitachi, m’Malawi muno munapangidwa mipingo yatsopano yokwana 49. Umenewutu ndi umboni wakuti Yehova akudalitsa ntchito yake m’gawo la nthambi yathu.