Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Ndife osangalala chifukwa cha kuwonjezeka kwa ofalitsa m’dziko lathu lino. M’mwezi wa July chaka chino, ofalitsa okwana 78,208 anapereka lipoti ndipotu zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri. Tiyenitu tipitirize kubzala mbewu za choonadi ndipo Yehova adzazikulitsa.—1 Akor. 3:6, 7.