Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi m’patseni kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? June: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. July ndi August: Gawirani kabuku kalikonse kamasamba 32 kamene anthu angachite nako chidwi m’gawo lanu pa timabuku iti: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndi kakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Ngati kuli koyenera, mungagawirenso kabuku kakuti Mverani Mulungu kapena kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo muyese kuyambitsa phunziro la Baibulo.