Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Muyesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. July ndi August: Ngati n’zotheka mungagawire timabuku iti m’gawo lanu: Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito timabukuti. Komanso mungagawire kabuku kalikonse kamene anthu angachite nako chidwi. September: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, mungayambitse phunziro la Baibulo pogwiritsira ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.