Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa January chaka chino tinathera maola okwana 1,219,526 mu utumiki wakumunda. Komatu m’mwezi umenewu chakudya chimakhala chovuta kupeza m’Malawi muno. Komanso, abale athu ambiri ali m’mavuto azachuma. Choncho, tikukuyamikirani kwambiri chifukwa chopitiriza kulalikira ndiponso kuphunzitsa anthu choonadi ngakhale mukukumana ndi mavuto ambiri m’masiku otsiriza ano.—Mat. 6:33.