Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Yehova akudalitsa ntchito yathu m’Malawi muno. Tikutero chifukwa m’chaka chautumiki cha 2012, mipingo 29 yatsopano inakhazikitsidwa m’dziko lathuli. Sitikukayikira kuti Mulungu wathu wabwino Yehova, apitiriza kudalitsa anthu ake ndi zinthu zambiri zabwino m’chaka chautumiki cha 2013 chimene chiyambe mu September. Tikukuthokozani abale ndi alongo nonse chifukwa choika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wanu.—Mal. 3:10; Mat. 6:33.