Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu November ndi December 2012: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa, Yehova—Kodi Iye Ndani? kapena Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. January ndi February 2013: Gawirani timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu kapena Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena ngati zili zoyenera mogwirizana ndi munthuyo, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.