Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Gawirani timabuku ta masamba 32 totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kapena kakuti, Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati zili zoyenerera mogwirizana ndi mwininyumbayo, gwiritsani ntchito kabuku kakuti, Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. March ndi April: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati zili zoyenerera mogwirizana ndi mwininyumbayo, gwiritsani ntchito kabuku kakuti, Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. May: Gawirani timapepala totsatirati: Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? kapena kakuti, Sangalalani ndi Moyo Wabanja. Munthu akachita chidwi, musonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, kabuku kakuti Mverani Mulungu, kapena kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha.
◼ Pakonzedwa autilaini yatsopano ya pa Chikumbutso ndipo kuyambira chaka chino cha 2013, abale onse amene azikamba nkhani pa Chikumbutso ayenera kugwiritsa ntchito autilaini imeneyi. Autilainiyi ili ndi mutu wakuti, “Muziyamikira Zimene Khristu Wakuchitirani.”
◼ Nkhani yapadera ya onse ya panyengo ya Chikumbutso cha 2013 ili ndi mutu wakuti, “Kodi Imfa ndi Mapeto a Zonse?”