Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso Mverani Mulungu ndi Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. November: Tidzagawira Uthenga wa Ufumu Na. 38 komanso buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? December: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? January: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu kapena Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha.
◼ Muzitenga Mabuku a Mpingo Wanu Wokha Pamalo Ofikira Mabuku: Muzionetsetsa kuti mwatenga makalata ndi mabuku a mpingo wanu wokha mukamatenga zinthu pamalo ofikira mabuku. Mungatenge zinthu za mpingo wina ngati abale a ku mpingowo akupemphani kuti muwatengere. Mukazindikira kuti mwatenga zinthu za mpingo wina mwangozi, tikukulimbikitsani kuti muzipititsa mwamsanga zinthuzo kumalo ofikira mabuku kapena muzitumiza mwamsanga ku mpingo womwe ukuyenera kulandira zinthuzo.