Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’Malawi muno muli mipingo 1,349 ndipo ofalitsa alipo 88,052. Pa mipingo imeneyi, mipingo 1,241 ndi ya Chichewa, 96 ya Chitumbuka, 47 ya Chitonga, 6 ya Chingelezi ndipo 5 ndi ya Chinenero Chamanja. Komanso pali magulu a Chinenero Chamanja m’malo ngati Nkhata Bay, Kasungu, Lilongwe Rural, Mchinji, Balaka, Mangochi, Zomba, Mulanje Boma, Migowi, Nchalo komanso m’madera ena. Tilinso ndi dera limodzi la Chinenero Chamanja, madera atatu a Chitonga, 5 a Chitumbuka ndiponso 53 a Chichewa. Madera onse alipo 62. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kudalitsa khama lathu pamene tikuyesetsa kulalikira uthenga wabwino m’madera onse a m’dziko muno.—Aroma 12:11.