Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu July: Gawirani timabuku totsatirati: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi kakuti, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! August: Tidzagwira ntchito yapadera yogawira kapepala kodziwitsa anthu za webusaiti yathu ya jw.org/ny. September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Kumbukirani kuti simuyenera kuchita misonkhano ya mpingo mlungu umene mudzachite msonkhano wachigawo. Zimenezi zimathandiza abale ndi alongo kukhala ndi nthawi yokwanira yokonzekera msonkhanowu. Mungasinthe ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki ya mlungu wotsatizana ndi mlungu wa msonkhano wanu wachigawo n’cholinga choti mukambiranenso nkhani zokhudza msonkhano zomwe zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno zakuti, “Khalani Ndi Khalidwe Labwino Pakati pa Anthu a M’dzikoli,” “Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Msonkhano” ndi yakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2014.” Mungakambiranenso malangizo okhudza kupewa ngozi omwe ali m’kalata yopita ku mipingo yonse ya pa August 3, 2013. Pakapita mwezi umodzi kapena iwiri mutachita msonkhano wachigawo, dzagwiritseni ntchito mbali ya zosowa za pampingo kukambirana mfundo za msonkhano wachigawo zimene ofalitsa aona kuti n’zothandiza mu utumiki.