Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Mpingo wa Mchenga Coal Mine uli ndi kagulu ka ofalitsa 13 omwe amakhala kufupi ndi ku Chiŵeta. Ngakhale kuti kaguluka sikanakhazikitsidwe kukhala kagulu kakutali, chaka chatha pa mwambo wa Chikumbutso womwe ofalitsawa anachita, panapezeka anthu 222. N’zosakayikitsa kuti anthuwa anaphunzira za chikondi chomwe Yehova anasonyeza pokonza zotiwombola ku uchimo ndi imfa. Tiyeni tiyesetse kuitana anthu ambiri kuti adzabwere pa Chikumbutso cha chaka chino, chomwe chidzachitike pa 3 April 2015.