Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 January tsamba 2
  • January 4-10

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January 4-10
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 January tsamba 2

January 4-10

2 MBIRI 29-32

  • Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Tiyenera Kuchita Khama Polambira Yehova”: (10 min.)

    • 2 Mbiri 29:10-17—Hezekiya analimba mtima kuti abwezeretse kulambira koona

    • 2 Mbiri 30:5, 6, 10-12—Hezekiya anaitana anthu a mtima wabwino kuti asonkhane polambira Yehova

    • 2 Mbiri 32:25, 26—Hezekiya anasintha n’kuyamba kudzichepetsa (w05 10/15 tsa. 25 ndime 20)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • 2 Mbiri 29:11—Kodi Hezekiya anasonyeza bwanji kuti anali chitsanzo chabwino posankha zochita (w13 11/15 tsa. 17 ndime 6-7)

    • 2 Mbiri 32:7, 8—Kodi tingatani pokonzekera mavuto amene tingakumanewo mtsogolo? (w13 11/15 tsa. 20 ndime 17)

    • Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

  • Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 31:1-10 (Osapitirira 4 min.)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Kukonzekera Zitsanzo za Ulaliki za Mwezi Uno. (15 min.) Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chosonyeza zimene tingachite pogawira magazini a Nsanja ya Olonda kenako kambiranani mfundo zimene mwaphunzirapo. Fotokozani zimene wofalitsa wachita kuti adzapange ulendo wobwereza. Chitani chimodzimodzi ndi chitsanzo chachiwiri chogawira Nsanja ya Olonda komanso kabuku ka Uthenga Wabwino. Onaninso mfundo zina pa mutu wakuti, “Kuphunzitsa Anthu Pogwiritsa Ntchito Kabuku ka Uthenga Wabwino.” Limbikitsani omvera kuti alembe zitsanzo za ulaliki zimene angakonde kugwiritsa ntchito pamalo amene apatsidwa.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 127

  • “Tizigwira Nawo Ntchito Yomanga Komanso Kukonza Malo Olambirira.” (15 min.) Nkhani yokambirana. Funsani abale ndi alongo amene anagwirako ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu kuti afotokoze zosangalatsa zimene anakumana nazo. Kenako funsani m’bale amene amayang’anira ntchito yoyeretsa komanso kukonza Nyumba ya Ufumu, kuti afotokoze mwachidule zimene mpingo unakonza zokhudza kusamalira nyumbayo.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 24 ndime 1-10 (30 min.)

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 142 ndi Pemphero

    Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena