July 25-31
MASALIMO 79-86
Nyimbo Na. 138 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu ndi Ndani?”: (10 min.)
Sal. 83:1-5—Cholinga chathu chachikulu chizikhala kulemekeza dzina la Yehova komanso ulamuliro wake (w08 10/15 13 ndime 7-8)
Sal. 83:16—Tikamakhalabe okhulupirika ngakhale pamavuto, dzina la Yehova limalemekezedwa (w08 10/15 15 ndime 16)
Sal. 83:17, 18—Yehova ndi wofunika kwambiri m’chilengedwe chonse (w11 5/15 16 ndime 1-2; w08 10/15 15-16 ndime 17-18)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 79:9—Kodi lemba limeneli lingatithandize bwanji kudziwa zimene tinganene m’mapemphero athu? (w06 7/15 12 ndime 5)
Sal. 86:5—Kodi Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka” motani? (w06 7/15 12 ndime 9)
Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 85:8–86:17
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) fg mutu 7 ndime 1
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) fg mutu 7 ndime 3
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) fg mutu 7 ndime 7-8
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?: (15 min.) Yambani ndi kuonera vidiyo yakuti Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina? (Kuti mupeze vidiyoyi, pitani pamene palembedwa kuti, MABUKU > MAVIDIYO. Kenako pitani pomwe pali kabuku ka Uthenga Wabwino. Vidiyoyi ikupezeka paphunziro 2 lakuti “Kodi Mulungu Ndani?”) Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vidiyoyi tikamalalikira mwamwayi, pamalo opezeka anthu ambiri komanso tikamalalikira kunyumba ndi nyumba? Kodi ndi zosangalatsa zotani zimene zinakuchitikirani pamene munkagwiritsa ntchito vidiyoyi?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 3 ndime 1-13, bokosi patsamba 29
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 143 ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse amvetsere, kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.