September 26–October 2
MASALIMO 142-150
Nyimbo Na. 134 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova ndi Wamkulu ndi Woyenera Kutamandidwa Kwambiri”: (10 min.)
Sal. 145:1-9—Ukulu wa Yehova ndi wosasanthulika (w04 1/15 10 ndime 3-4; 11 ndime 7-8; 14 ndime 20-21; 15 ndime 2)
Sal. 145:10-13—Atumiki a Yehova okhulupirika amayesetsa kumutamada (w04 1/15 16 ndime 3-6)
Sal. 145:14-16—Yehova amafunitsitsa kuthandiza atumiki ake (w04 1/15 17-18 ndime 10-14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 143:8—Kodi lembali lingatithandize bwanji kuti tizilemekeza Yehova tsiku lililonse? (w10 1/15 21 ndime 1-2)
Sal. 150:6—Kodi lemba lomaliza la m’buku la Masalimo limatsindika mfundo yotani? (w13 11/15 4 ndime 4; it-2-E 448)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 145:1-21
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) 1 Pet. 5:7—Kuphunzitsa Choonadi.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Sal. 37:9-11—Kuphunzitsa Choonadi.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) fg phunziro 9 ndime 3—Thandizani wophunzira wanu kuti azigwiritsa ntchito zimene waphunzira.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizilimbikitsa Anthu Achidwi Kuti Azifika Kumisonkhano Yathu”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Konzani zoti pagawidwe timapepala toitanira anthu kumisonkhano yathu ndipo kenako kambiranani mwachidule tsamba 2. Onetsani vidiyo yosonyeza wofalitsa akuitanira munthu amene amamupatsa magazini kumisonkhano yathu. Pomaliza kambiranani kabokosi kakuti, “Zomwe Tidzagawire mu October: Kapepala Koitanira Anthu Kumisonkhano.”
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 7 ndime 15-27, Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 66
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 145 ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo.