March 20-26
YEREMIYA 8-11
Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anthu Akamatsogoleredwa ndi Yehova Zinthu Zimawayendera Bwino”: (10 min.)
Yer. 10:2-5, 14, 15—Milungu ya anthu a mitundu ina ndi yonyenga (w03 5/1 15 ¶5; it-1-E 555)
Yer. 10:6, 7, 10-13—Mosiyana ndi milungu ya anthu a mitundu ina, Yehova yekha ndiye Mlungu woona (w04 10/1 11 ¶10)
Yer. 10:21-23—Ngati anthu satsogoleredwa ndi Yehova zinthu sizimawayendera bwino (w15 9/1 15 ¶1)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yer. 9:24—Kodi ndi kunyada ndiponso kudzitamanda kotani komwe ndi kwabwino? (w13 1/15 20 ¶16)
Yer. 11:10—N’chifukwa chiyani Yeremiya anaphatikiza ufumu wakumpoto wa mafuko 10 mu uthenga wake ngakhale kuti Samariya anali atawonongedwa kale mu 740 B.C.E.? (w07 3/15 9 ¶2)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 11:6-16
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso ndiponso wp17.2 chikuto—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso wp17.2 chikuto—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) ld tsamba 4-5 (Wofalitsa angasankhe zithunzi zomwe akufuna kukambirana.)—Muitanireni ku Chikumbutso.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Mverani Mulungu?”: (15 min.) Yambani ndi kukambirana nkhaniyi kwa maminitsi 5. Kenako onetsani ndiponso kukambirana vidiyo imene ikusonyeza munthu akuphunzira Baibulo ndi munthu wina pogwiritsa ntchito tsamba 8 ndi 9 la kabukuka. M’vidiyoyi wophunzira akugwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu pomwe wofalitsa akugwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Limbikitsani abale ndi alongo kuti atenge kabuku kawo ka Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha n’kumatsatira vidiyoyi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 20 ¶1-13
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero