Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 December tsamba 7
  • Chikondi Chenicheni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Chenicheni
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Tetezani Banja Lanu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mungapeze Nzeru Zokuthandizani pa JW.ORG
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 December tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Chikondi Chenicheni

Yehova poyambitsa ukwati, anafuna kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana azikhala limodzi kwa moyo wonse. (Gen. 2:22-24) Munthu angasankhe kuthetsa ukwati pokhapokha ngati wina wachita chigololo. (Mal. 2:16; Mat. 19:9) Popeza Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azikhala mosangalala, anapereka malangizo othandiza Akhristu kuti azitha kusankha bwino munthu wokwatirana naye n’cholinga choti akhale ndi mabanja abwino.​—Mlal. 5:4-6.

ONERANI VIDIYO YAKUTI CHIKONDI CHENICHENI KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Liz akucheza ndi bambo ake

    N’chifukwa chiyani malangizo omwe Liz analandira kwa bambo ndi mayi ake ali anzeru komanso othandiza?

  • N’chifukwa chiyani si nzeru kuganiza kuti mungathe kusintha khalidwe la munthu amene muli naye pa chibwenzi?

  • Kodi m’bale ndi mlongo Foster anapereka malangizo otani kwa Liz?

  • Zack ndi Magi ali ku Nyumba ya Ufumu

    Kodi mavuto anayamba bwanji m’banja la Zack ndi Magi?

  • Liz ndi John ali ku Nyumba ya Ufumu

    Kodi John ndi Liz anali ndi zolinga zauzimu ziti zomwe zinali zofanana?

  • N’chifukwa chiyani musanakwatirane mumafunika kudziwa “munthu wobisika wamumtima” wa munthu amene mukufuna kukwatirana naye? (1 Pet. 3:4)

  • Kodi chikondi chenicheni tingachidziwe bwanji? (1 Akor. 13:4-8)

Kodi Akhristu angapeze kuti mfundo zina zothandiza pa nkhani zokhudza chibwenzi?

  • Mavidiyo a pa JW Broadcasting akuti Kukonzekera Banja

  • Vidiyo ya pa JW.ORG yakuti Kodi Ndi Chikondi Chenicheni Kapena Kungotengeka Maganizo?

  • Buku loyamba ndi lachiwiri la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa

  • Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani (Pitani pamene alemba kuti “Moyo Wabanja,” kenako pamene alemba kuti “Kupeza Chibwenzi.”)

Kodi okwatirana angapeze kuti malangizo othandiza kuti banja lawo liziyenda bwino?

  • Nkhani za pa JW. ORG (Pitani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MALANGIZO OTHANDIZA BANJA LONSE.)

  • Kabuku kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala

  • Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja

  • Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani (Pitani pamene alemba kuti “Moyo Wabanja,” kenako pamene alemba kuti “Banja.”)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena