January 14-20
MACHITIDWE 23-24
Nyimbo Na. 148 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anaimbidwa Mlandu Wosokoneza Anthu Komanso Kuukira Boma”: (10 min.)
Mac. 23:12, 16—Chiwembu chofuna kupha Paulo chinalephereka (bt 191 ¶5-6)
Mac. 24:2, 5, 6—Munthu wina wodziwa kulankhula, dzina lake Teritulo, analankhula zoipa zokhudza Paulo kwa bwanamkubwa wachiroma (bt 192 ¶10)
Mac. 24:10-21—Paulo anakana mwaulemu milandu yomwe anamunamizira ndipo anachitira umboni molimba mtima (bt 193-194 ¶13-14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mac. 23:6—N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti anali Mfarisi? (“ine ndine Mfarisi” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 23:6, nwtsty)
Mac. 24:24, 27—Kodi Durusila anali ndani? (“Durusila” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 24:24, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 23:1-15 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri. (th phunziro 2)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri. (th phunziro 3)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lipoti la Chaka Chautumiki: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pambuyo powerenga chilengezo chochokera ku ofesi ya nthambi chokhudza lipoti la chaka chautumiki, funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo muutumiki chaka chathachi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 21
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero