April 1-7
1 AKORINTO 7-9
Nyimbo Na. 136 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kusakhala Pabanja ndi Mphatso”: (10 min.)
1 Akor. 7:32—Akhristu omwe sali pabanja amatumikira Yehova popanda kuda nkhawa ndi mavuto amene anthu apabanja amakumana nawo (w11 1/15 18 ¶3)
1 Akor. 7:33, 34—Akhristu omwe ali pabanja “amadera nkhawa zinthu za dziko” (w08 7/15 27 ¶1)
1 Akor. 7:37, 38—Akhristu omwe asankha kusakhala pabanja n’cholinga choti achite zambiri potumikira Yehova ‘amachita bwino koposa’ amene ali pabanja (w96 10/15 12-13 ¶14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Akor. 7:11—Kodi n’chiyani chingachititse Mkhristu kusankha kuti apatukane ndi mwamuna kapena mkazi wake? (lvs 251)
1 Akor. 7:36—N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kulowa m’banja ‘akapitirira pachimake pa unyamata’? (w00 7/15 31 ¶2)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Akor. 8:1-13 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba, kenako kambiranani phunziro 4 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w12 11/15 20—Mutu: Kodi Anthu Amene Amasankha Kusakhala Pabanja Amalandira Mphatsoyi M’njira Yapadera? (th phunziro 12)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi Yomwe Simuli Pabanja: (15 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi Akhristu amene sali pabanja amakumana ndi mavuto otani? (1 Akor. 7:39) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mwana wa Yefita ndi chitsanzo chabwino? Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu amene amakhalabe okhulupirika? (Sal. 84:11) Kodi abale ndi alongo mumpingo angalimbikitse bwanji Akhristu omwe sali pabanja? Kodi Akhristu omwe sali pabanja ali ndi mwayi wochita mautumiki ati?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 32
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero