May 6-12
2 Akorinto 4-6
Nyimbo Na. 128 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Sitikubwerera M’mbuyo”: (10 min.)
2 Akor. 4:16—“Tsiku ndi tsiku” Yehova amatithandiza kukhalanso atsopano (w04 8/15 25 ¶16-17)
2 Akor. 4:17—Mavuto omwe tikukumana nawowa ndi ‘akanthawi komanso opepuka’ (it-1 724-725)
2 Akor. 4:18—Tiziganizira madalitso a Ufumu omwe tidzapeze mtsogolo
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
2 Akor. 4:7—Kodi chuma chomwe chili “m’zonyamulira zoumbidwa ndi dothi” n’chiyani? (w12 2/1 28-29)
2 Akor. 6:13—Kodi tingatsatire bwanji malangizo akuti “futukulani mtima wanu”? (w09 11/15 21 ¶7)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 2 Akor. 4:1-15 (th phunziro 12)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kuwerenga Molondola, kenako kambiranani phunziro 5 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w04 7/1 30-31—Mutu: Kodi Mkhristu Wobatizidwa Angakhale pa Chibwenzi ndi Wofalitsa Wosabatizidwa? (th phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Ndimachita Zonse Zomwe Ndingathe: (8 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi m’bale Foster anasonyeza bwanji kuti anadzipereka kwambiri potumikira Yehova ali wachinyamata? Kodi zinthu zinasintha bwanji pa moyo wake? Kodi panopa akuchita zotani potumikira Yehova ngakhale kuti zinthu zinasintha pa moyo wake? Kodi mwaphunzira zotani pa zomwe zinachitikira m’bale Foster?
Zofunika Pampingo: (7 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 35 ¶20-27 ndi bokosi lakuti “Ankabwereza Mfundo Pophunzitsa”
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero