July 1-7
AKOLOSE 1-4
Nyimbo Na. 56 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Vulani Umunthu Wakale N’kuvala Umunthu Watsopano”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Akolose.]
Akol. 3:5-9—“Vulani umunthu wakale” (w11 3/15 10 ¶12-13)
Akol. 3:10-14—“Muvale umunthu watsopano” (w13 9/15 21 ¶18-19)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Akol. 1:13, 14—Kodi “ufumu wa Mwana wake wokondedwa” n’chiyani? (it-2 169 ¶3-5)
Akol. 2:8—Kodi “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” n’chiyani? (w08 8/15 28 ¶9)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Akol. 1:1-20 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima, kenako kambiranani phunziro 7 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w04 5/1 19-20 ¶3-7—Mutu: Kodi Akhristu ena ‘anathandiza komanso kulimbikitsa’ Paulo m’njira yotani? (Akol. 4:11) (th phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lipoti Lochokera ku Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa la 2018: (15 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani tinganene kuti masiku ano nkhani ya maulendo ndi yofunika kwambiri m’gulu lathu? Kodi Dipatimenti Yoona za Maulendo yathandiza bwanji kupulumutsa ndalama za gulu la Yehova? Kodi ofalitsa angathandize bwanji kuti gulu lisamawononge ndalama zambiri? Kodi a m’Dipatimenti Yoona za Maulendo adzathandiza bwanji alendo ochokera m’mayiko osiyanasiyana akamadzapita kukachita msonkhano wa mayiko mu 2019?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 42
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero