September 9-15
AHEBERI 9-10
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Chithunzi cha Zinthu Zabwino Zimene Zikubwera”: (10 min.)
Aheb. 9:12-14—Magazi a Khristu ndi apamwamba kwambiri kuposa a mbuzi komanso a ng’ombe (it-1 862 ¶1)
Aheb. 9:24-26—Khristu anakapereka mtengo wa nsembe yake kwa Mulungu ndipo anachita zimenezi kamodzi kokha (cf 183 ¶4)
Aheb. 10:1-4—Chilamulo chinkaimira zinthu zabwino zimene zikubwera m’tsogolo (it-2 602-603)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Aheb. 9:16, 17—Kodi mavesiwa akutanthauza chiyani? (w92 3/1 31 ¶4-6)
Aheb. 10:5-7—Kodi ndi liti pamene Yesu analankhula mawu amenewa, nanga ankatanthauza chiyani? (it-1 249-250)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Aheb. 9:1-14 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 2)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako musiyireni khadi lodziwitsa anthu za jw.org. (th phunziro 11)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Timayamikira Misonkhano Yathu? (Sal. 27:11): (12 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:
Kodi ndi zinthu ziti zomwe Yesu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe, akutichitira masiku ano?
Kodi tingasonyeze kuyamikira m’njira zitatu ziti?
Muzimvetsera Pamisonkhano: (3 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako pemphani ana kuti afotokoze chifukwa chake ayenera kumamvetsera akakhala pamisonkhano.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 50
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 128 ndi Pemphero