January 20-26
GENESIS 6-8
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anachitadi Momwemo”: (10 min.)
Gen. 6:9, 13—Nowa anali wolungama koma ankakhala pakati pa anthu oipa (w18.02 4 ¶4)
Gen. 6:14-16—Nowa anapatsidwa ntchito yovuta (w13 4/1 14 ¶1)
Gen. 6:22—Nowa ankakhulupirira Yehova (w11 9/15 18 ¶13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 7:2—Kodi zinyama anazisiyanitsa kuti zina ndi zodetsedwa pomwe zina n’zosadetsedwa potengera mfundo yotani? (w04 1/1 29 ¶7)
Gen. 7:11—Kodi madzi amene anachititsa Chigumula padziko lonse anachokera kuti? (w04 1/1 30 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 6:1-16 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi wofalitsa wagwiritsa ntchito bwanji lemba la 1 Yohane 4:8, pokambirana ndi mwininyumba? Kodi ofalitsawa anathandizana bwanji pomulalikira munthuyu?
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Kenako mugawireni chilichonse cha zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa. (th phunziro 7)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kulambira kwa Pabanja—Nowa Anayenda ndi Mulungu: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi m’vidiyoyi, makolo anagwiritsa ntchito bwanji nkhani ya m’Baibulo ya Nowa pophunzitsa ana awo? Kodi ndi mfundo zabwino ziti zomwe mungazigwiritse ntchito pa kulambira kwanu kwa pa banja?
Zofunika Pampingo: (5 min.)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 69
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 40 ndi Pemphero