February 24–March 1
GENESIS 20-21
Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Amakwaniritsa Zomwe Walonjeza”: (10 min.)
Gen. 21:1-3—Sara anatenga pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna (wp17.5 14-15)
Gen. 21:5-7—Yehova anapangitsa zinthu zomwe zinkaoneka ngati zosatheka kukhala zotheka
Gen. 21:10-12, 14—Abulahamu ndi Sara ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova okhudza Isaki
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 20:12—Kodi Sara anali mlongo wake wa Abulahamu m’njira yotani? (wp17.3 12, mawu a m’munsi.)
Gen. 21:33—Kodi Abulahamu anaitanira bwanji pa “dzina la Yehova”? (w89 7/1 20 ¶9)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 20:1-18 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi wofalitsayu wathandiza bwanji munthuyo kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo ya palemba lomwe awerenga? N’chifukwa chiyani tinganene kuti imeneyi ndi njira yabwino yothandizira munthu amene wasonyeza chidwi?
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (th phunziro 4)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) bhs 35 ¶19-20 (th phunziro 3)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lipoti la Chaka Chautumiki: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pambuyo powerenga chilengezo chochokera ku ofesi ya nthambi chokhudza lipoti la chaka chautumiki, funsani ofalitsa omwe munawasankhiratu kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo mu utumiki chaka chathachi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 74
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 100 ndi Pemphero