June 15-21
GENESIS 48-50
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Achikulire Angatiphunzitse Zambiri”: (10 min.)
Gen. 48:21, 22—Yakobo anali ndi chikhulupiriro kuti Aisiraeli adzalanda dziko la Kanani (it-1 1246 ¶8)
Gen. 49:1—Ulosi umene Yakobo analosera atatsala pang’ono kufa unasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro (it-2 206 ¶1)
Gen. 50:24, 25—Yosefe anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza (w07 6/1 28 ¶10)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 49:19—Kodi zimene Yakobo analosera zokhudza Gadi zinakwaniritsidwa bwanji? (w04 6/1 15 ¶4-5)
Gen. 49:27—Kodi zimene Yakobo analosera zokhudza Benjamini zinakwaniritsidwa bwanji? (it-1 289 ¶2)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 49:8-26 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi ofalitsawa anachitira bwanji zinthu limodzi mogwirizana polalikira? Kodi tingatsanzire bwanji ofalitsawa posonyeza kuti timakhulupirira zimene tikunena tikakhala mu utumiki?
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 6)
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako mugawireni buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndipo yambitsani phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito mutu 9 (th phunziro 16)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Zimene Tingaphunzire kwa Akhristu Omwe Atumikira kwa Nthawi Yaitali”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kukhalabe Ogwirizana Panthawi Imene Ntchito Yathu Inali Yoletsedwa.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 88 ndime 1-11
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 61 ndi Pemphero