MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mungathe Kulalikira Komanso Kuphunzitsa
Mose atangopatsidwa kumene utumiki ndi Yehova, ankadziona kuti sangakwanitse. (Eks. 4:10, 13) Kodi inunso munayamba mwamvapo choncho? Kodi mukuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova? Kodi mumadzifunsa ngati mungakwanitse kulalikira kunyumba ndi nyumba? Kapena ndinu wachinyamata ndipo mumachita mantha kulalikira kusukulu. Kapenanso mwina mumachita mantha kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri kapena kuchita ulaliki wa patelefoni. Pemphani Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera. (1 Pet. 4:11) Muzikhulupirira kuti angakuthandizeni kukwaniritsa utumiki uliwonse umene wakupatsani.—Eks. 4:11, 12.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU MOLIMBA MTIMA—OFALITSA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Mlongo Aoyama anakumana ndi vuto lotani?
N’chiyani chinamuthandiza kupeza mphamvu komanso kukhala olimba mtima?—Yer. 20:7-9
Kodi kuchita zambiri potumikira Yehova kunamuthandiza bwanji?
Kodi Yehova angakuthandizeni kuthana ndi mavuto ati mukamalalikira?