August 31–September 6
EKISODO 21-22
Nyimbo Na. 141 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muzisonyeza Kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonera”: (10 min.)
Eks 21:22, 23—Yehova amaona kuti moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali (lvs 95 ¶16)
Eks 21:28, 29—Yehova amafuna kuti tizichita zinthu mosamala kuti tizipewa ngozi (w10 4/15 29 ¶4)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 21:5, 6—Kodi mavesiwa akusonyeza bwanji kuti kudzipereka kwa Yehova n’kothandiza? (w10 1/15 4 ¶4-5)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 21:1-21 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako muitanireni kumisonkhano yathu. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako musonyezeni ndi kukambirana naye mfundo za m’vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (koma musaonetse vidiyoyi). (th phunziro 20)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w09 4/1 31—Mutu: Yehova Ndi Atate wa Ana Amasiye. (th phunziro 19)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziona Moyo Mmene Yehova Amauonera: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani mafunso awa: Ndi mavuto otani amene mayi angakumane nawo akakhala woyembekezera? Mogwirizana ndi Ekisodo 21:22, 23, kodi nkhani yochotsa mimba timaiona bwanji? N’chifukwa chiyani chikhulupiriro komanso kulimba mtima n’zofunika kuti tisankhe kuchita zinthu zosangalatsa Yehova? Kodi chiyembekezo chakuti akufa adzauka chimatilimbikitsa bwanji?
Mmene Kudzipereka Kumatithandizira: (5 min.) Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2010, tsamba 4, ndime 4-7. Limbikitsani ophunzira Baibulo kuti afike podzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 98
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero