May 24-30
NUMERI 34-36
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Thawirani kwa Yehova”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Nu 35:31—N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava sadzapindula nawo ndi nsembe ya dipo ya Yesu? (w91 2/15 13 ¶13)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Nu 34:1-15 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (th phunziro 9)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) fg phunziro 2 ¶9-10 (th phunziro 19)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 88
Khalani Bwenzi la Yehova—Amatilangiza Chifukwa Chotikonda: (6 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako ngati n’zotheka, funsani ana omwe munawasankhiratu mafunso awa: N’chifukwa chiyani nthawi zina mumafunika kupatsidwa malangizo? Kodi malangizo amakuthandizani bwanji? N’chifukwa chiyani Yehova amapereka malangizo?
“Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda”: (9 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti “Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.”
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 135
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero