March 14-20
1 SAMUELI 14-15
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kumvera Kumaposa Nsembe”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 1Sa 15:1-16 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Ulendo Wobwereza: Yesu—Mt 20:28. Muziimitsa vidiyoyi nthawi iliyonse imene pali chizindikiro chosonyeza kuti muime n’kufunsa omvera mafunso omwe ali muvidiyoyi.
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Gawirani chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 3)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo, ndipo yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? (th phunziro 11)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba Loweruka pa 19 March: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onani mwachidule zimene zili pa kapepala koitanira ku Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza zokhudza kudzamvetsera nkhani yapadera ndi mwambo wa Chikumbutso komanso zomwe mudzachite kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu. Onerani ndi kukambirana vidiyo ya zimene tinganene pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso.
Khalani Bwenzi la Yehova—Muzimvera Yehova: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 13 ndime 13-22, mawu akumapeto 28, 29
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero