January 23-29
1 MBIRI 4-6
Nyimbo Na. 42 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mapemphero Anga Amasonyeza Kuti Ndine Wotani?”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
1Mb 5:10—Kodi kugonjetsedwa kwa Ahagara kungatilimbikitse bwanji tikakumana ndi mavuto amene akuoneka ngati aakulu kwambiri? (w05 10/1 9 ¶7)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 1Mb 6:61-81 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 3)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 14)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) lff phunziro 08 zomwe taphunzira, kubwereza ndi zolinga (th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzikonzekereratu Panopa Zimene Mudzachite Mukadzadwala”: (15 min.) Vidiyo komanso nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Mukhale ndi nthawi yokwanira yoti abale ndi alongo ambiri apereke ndemanga pambuyo poonera vidiyoyi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 35
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero