Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 July tsamba 6-7
  • July 22-28

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • July 22-28
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 July tsamba 6-7

JULY 22-28

MASALIMO 66-68

Nyimbo Na. 7 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku Lililonse

(10 min.)

Yehova amamvetsera tikamapemphera ndipo amatiyankha (Sl 66:19; w23.05 12 ¶15)

Yehova amadziwa bwino zimene anthu amene akukumana ndi mavuto amafunikira (Sl 68:5; w10 12/1 23 ¶6; w09 4/1 31 ¶1)

Yehova amatithandiza tsiku lililonse (Sl 68:19; w23.01 19 ¶17)

Zithunzi zosonyeza mlongo akupemphera pa nthawi zosiyanasiyana: 1. M’mawa atangodzuka kumene. 2. Ndi ana ake asanapite kusukulu. 3. Kuntchito.

FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi timalola bwanji Yehova kuti atinyamulire katundu wathu?

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 68:18—M’nthawi ya Aisiraeli akale, kodi ‘anatenga amuna ati kuti akhale mphatso’? (w06 6/1 10 ¶5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 66:1-20 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba ndi wa chikhalidwe chosiyana ndi chanu. (lmd phunziro 5 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitirizani kukambirana za kapepala komwe munamusiyira pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 3)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 15 mawu oyamba komanso mfundo 1-3 (th phunziro 8)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 102

7. Kodi Munganyamuleko Katundu wa Munthu Wina?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Palibe mtumiki wa Mulungu aliyense amene angalimbane ndi mavuto payekha. (2Mb 20:15; Sl 127:1) Yehova ndi amene amatithandiza. (Yes 41:10) Kodi Yehova amatithandiza bwanji? Amatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake komanso m’gulu lake. (Yes 48:17) Amatipatsa mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu. (Lu 11:13) Komanso amachititsa abale ndi alongo athu kuti atilimbikitse komanso atithandize. (2Ak 7:6) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova akhoza kugwiritsa ntchito aliyense wa ife kuti anyamuleko katundu wa Mkhristu mnzake.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu​—⁠Muzikonda Achikulire.” Mlongo Paulina Sántiz Gómez ali panja panyumba yake ndipo akumwetulira.

Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Achikulire. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa Mkhristu wachikulire?

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu​—⁠Muzikonda Amene Akuchita Utumiki wa Nthawi Zonse.” Joseph ndi Anita DeVito ali limodzi mu utumiki.

Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Amene Akuchita Utumiki wa Nthawi Zonse. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa amene akuchita utumiki wa nthawi zonse?

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu​—⁠Muzikonda Anthu Ochokera Kumayiko Ena.” Bill ndi Maggie Zeng akumwetulira pamene akuphunzira Baibulo.

Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Anthu Ochokera Kumayiko Ena. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa amene akukumana ndi mayesero aakulu?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 13 ¶1-7, mawu ofotokoza gawo 5 ndi bokosi patsamba 103

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena