Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 November tsamba 10-11
  • December 16-22

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 16-22
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 November tsamba 10-11

DECEMBER 16-22

SALIMO 119:57-120

Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Zimene Tingachite Kuti Tizipirira Mavuto

(10 min.)

Tizipitiriza kuwerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu (Sl 119:61; w06 6/15 20 ¶2; w00 12/1 14 ¶3)

Tizilola kuti mavutowo atiyenge (Sl 119:71; w06 9/1 14 ¶4)

Tizidalira Yehova kuti atilimbikitse (Sl 119:76; w17.07 13 ¶3, 5)

M’bale amene akudwala wakhala pabedi ndipo akupemphera limodzi ndi mkazi wake.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova wandithandiza kupirira mavuto anga m’njira ziti?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 119:96—Kodi n’kutheka kuti vesili limatanthauza chiyani? (w06 9/1 14 ¶5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 119:57-80 (th phunziro 12)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Musonyezeni webusaiti yathu ya jw.org ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za webusaitiyi. (lmd phunziro 2 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni kuti adzamvetsere nkhani ya onse yotsatira. Gwiritsani ntchito vidiyo yamutu wakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (lmd phunziro 8 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Chitsanzo. ijwbq 157—Mutu: Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zam’chilengedwe? (lmd phunziro 3 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 128

7. Yehova Amatithandiza Kupirira

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Kupirira kumatanthauza kusagonja tikakumana ndi mavuto. Kumaphatikizapo kukhalabe wolimba, kupitiriza kuona zinthu moyenera komanso kukhala ndi chiyembekezo kuti mayeserowo atha. Mkhristu akakhala wopirira, ‘sabwerera m’mbuyo’ kapena kufooka akakumana ndi mavuto. (Ahe 10:36-39) Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza kupirira mayesero.—Ahe 13:6.

Pa lemba lililonse mwa malemba omwe ali m’munsiwa, lembani mmene Yehova amatithandizira kupirira.

  • Lu 11:13

  • Aro 8:25

  • 1At 5:11

  • Yak 1:5

Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzipempherera Anthu Amene Akukumana ndi Mavuto.” 1. Banja la a Wilson likuchita kulambira kwa pabanja pogwiritsa ntchito zochita za mutu wakuti “Khalani Bwenzi la Yehova—Uzipempherera Ena.” 2. A Glynis akupemphera.

Onerani VIDIYO yakuti Muzipempherera Anthu Amene Akukumana ndi Mavuto. Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • Kodi tingagwiritse ntchito bwanji jw.org kuti tidziwe zokhudza abale ndi alongo athu amene akukumana ndi mayesero?

  • Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azipempherera ena, nanga ubwino wake ndi wotani?

  • Kodi kupempha Yehova kuti athandize Akhristu anzathu kupirira n’kofunika bwanji?

  • Kodi kupempherera ena kungatithandize bwanji kupirira mayesero amene tikukumana nawo?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 19 ¶14-20, bokosi patsamba 152

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena