Kodi Kupemphera N’kothandizadi?
© 2020 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka ndalama, pitani pa donate.jw.org. Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.
MAGAZINI ya Nsanja ya Olonda imalemekeza Yehova Mulungu, yemwe ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchotsa zoipa zonse n’kusintha dziko lapansili kukhala Paradaiso. Imalimbikitsanso anthu kukhulupirira Yesu Khristu yemwe anatifera kuti tidzapeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambira mu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zake zimachokera m’Baibulo.