Magazini Yophunzira
FEBRUARY 2021
NKHANI ZOPHUNZIRA KUYAMBIRA: APRIL 5–MAY 2, 2021
© 2020 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka pitani pa donate.jw.org.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.
CHITHUNZI CHAPACHIKUTO:
Abigayeli atatumiza chakudya kwa Davide ndi asilikali ake, anapita kukakumana ndi Davideyo. Kenako anagwada pansi n’kumuchonderera kuti asadzibweretsere mlandu wa magazi pobwezera (Onani nkhani yophunzira 6, ndime 16)