Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 March tsamba 32
  • Kukhululuka Machimo Amene Anachitika Kale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhululuka Machimo Amene Anachitika Kale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Tiziyamikira Mphatso ya Dipo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Dipo Limasonyeza Bwino Chilungamo cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 March tsamba 32

MAWU A M’BAIBULO

Kukhululuka Machimo Amene Anachitika Kale

Njira yokhayo imene machimo athu angakhululukidwe ndi kudzera mu nsembe imene Yesu anapereka pogwiritsa ntchito magazi ake. (Aef. 1:7) Komabe Baibulo limati: “Mulungu . . . anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale,” kutanthauza Yesu asanapereke dipo. (Aroma 3:25) Koma kodi Yehova anachita bwanji zimenezi pa nthawi imodzimodziyo n’kusonyeza chilungamo chake?

Kwa Yehova zinali ngati dipo laperekedwa kale kungochokera pamene anaganiza zosankha “mbadwa” yoti idzapulumutse anthu. (Gen. 3:15; 22:18) Mulungu sankakayikira ngakhale pang’ono kuti pa nthawi yake, Mwana wake wokondedwa adzapereka moyo wake monga dipo. (Agal. 4:4; Aheb. 10:7-10) Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zotha kukhululuka machimo ngakhale pamene dipo linali lisanaperekedwe. Yesu ankakhululukira anthu omwe anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chifukwa ankadziwa kuti dipo lomwe adzapereke lidzaphimba machimo awo.​—Mat. 9:2-6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena