2 MAFUMU
ZIMENE ZILI MʼBUKULI
1
2
Eliya anatengedwa ndi mphepo yamkuntho (1-18)
Elisa anachititsa kuti madzi a ku Yeriko akhale abwino (19-22)
Zimbalangondo zinapha anyamata a ku Beteli (23-25)
3
Yehoramu, mfumu ya Isiraeli (1-3)
Amowabu anagalukira Isiraeli (4-25)
Amowabu anagonjetsedwa (26, 27)
4
Elisa anachulukitsa mafuta a mkazi wamasiye (1-7)
Mtima wochereza wa mayi wa ku Sunemu (8-16)
Mayi anakhala ndi mwana; mwanayo anamwalira (17-31)
Elisa anaukitsa mwana (32-37)
Elisa anachotsa poizoni mʼchakudya (38-41)
Elisa anachulukitsa mikate (42-44)
5
6
7
Elisa analosera za kutha kwa njala (1, 2)
Chakudya chinangosiyidwa mumsasa wa Asiriya (3-15)
Ulosi wa Elisa unakwaniritsidwa (16-20)
8
Mayi wa ku Sunemu anabwezeredwa malo ake (1-6)
Elisa, Beni-hadadi ndi Hazaeli (7-15)
Yehoramu, mfumu ya Yuda (16-24)
Ahaziya, mfumu ya Yuda (25-29)
9
Yehu anadzozedwa kukhala mfumu ya Isiraeli (1-13)
Yehu anapha Yehoramu ndi Ahaziya (14-29)
Yezebeli anaphedwa; agalu anadya thupi lake (30-37)
10
Yehu anapha anthu amʼbanja la Ahabu (1-17)
Yehu anapha anthu olambira Baala (18-27)
Ulamuliro wa Yehu (28-36)
11
Ataliya analanda ufumu (1-3)
Yehoasi anavekedwa ufumu mobisa (4-12)
Ataliya anaphedwa (13-16)
Yehoyada anasintha zinthu (17-21)
12
Yehoasi mfumu ya Yuda (1-3)
Yehoasi anakonza kachisi (4-16)
Asiriya anaukira (17, 18)
Yehoasi anaphedwa (19-21)
13
Yehoahazi mfumu ya Isiraeli (1-9)
Yehoasi mfumu ya Isiraeli (10-13)
Elisa anayesa khama la Yehoasi (14-19)
Elisa anamwalira; mafupa ake anaukitsa munthu (20, 21)
Ulosi womaliza wa Elisa unakwaniritsidwa (22-25)
14
Amaziya, mfumu ya Yuda (1-6)
Amaziya anamenyana ndi Aedomu ndi Aisiraeli (7-14)
Imfa ya Yehoasi wa ku Isiraeli (15, 16)
Imfa ya Amaziya (17-22)
Yerobowamu Wachiwiri, mfumu ya Isiraeli (23-29)
15
Azariya, mfumu ya Yuda (1-7)
Mafumu omaliza a Yuda: Zekariya (8-12), Salumu (13-16), Menahemu (17-22), Pekahiya (23-26), Peka (27-31)
Yotamu, mfumu ya Yuda (32-38)
16
Ahazi, mfumu ya Yuda (1-6)
Ahazi anapereka ziphuphu kwa Asuri (7-9)
Ahazi anatengera mapulani a guwa la mulungu wonama (10-18)
Imfa ya Ahazi (19, 20)
17
Hoshiya, mfumu ya Isiraeli (1-4)
Kugonjetsedwa kwa Isiraeli (5, 6)
Aisiraeli anapita ku ukapolo chifukwa cha mpatuko (7-23)
Anthu a mitundu ina anabweretsedwa mʼmizinda ya ku Samariya (24-26)
Ku Samariya kunali zipembedzo zosiyanasiyana (27-41)
18
Hezekiya, mfumu ya Yuda (1-8)
Kugonjetsedwa kwa ufumu wa Isiraeli (9-12)
Senakeribu anaukira Yuda (13-18)
Rabisake ananyoza Yehova (19-37)
19
Hezekiya anapempha thandizo kwa Yehova kudzera mwa Yesaya (1-7)
Senakeribu anaopseza Yerusalemu (8-13)
Pemphero la Hezekiya (14-19)
Yesaya anafotokoza zimene Mulungu anayankha (20-34)
Mngelo anapha Asuri 185,000 (35-37)
20
Hezekiya anadwala nʼkuchira (1-11)
Anthu anatumidwa kuchokera ku Babulo (12-19)
Imfa ya Hezekiya (20, 21)
21
Manase, mfumu ya Yuda; anapha anthu (1-18)
Amoni, mfumu ya Yuda (19-26)
22
Yosiya, mfumu ya Yuda (1, 2)
Malangizo okhudza kukonza kachisi (3-7)
Anapeza buku la Chilamulo (8-13)
Hulida analosera tsoka (14-20)
23
Yosiya anasintha zinthu (1-20)
Anachita chikondwerero cha Pasika (21-23)
Zinthu zinanso zimene Yosiya anasintha (24-27)
Imfa ya Yosiya (28-30)
Yehoahazi, mfumu ya Yuda (31-33)
Yehoyakimu, mfumu ya Yuda (34-37)
24
Kugalukira kwa Yehoyakimu komanso imfa yake (1-7)
Yehoyakini, mfumu ya Yuda (8, 9)
Ayuda oyamba kupita ku Babulo (10-17)
Zedekiya, mfumu ya Yuda; anagalukira (18-20)
25
Nebukadinezara anazungulira Yerusalemu (1-7)
Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa; Ayuda enanso anapita ku Babulo (8-21)
Gedaliya anaikidwa kuti azilamulira (22-24)
Gedaliya anaphedwa; anthu anathawira ku Iguputo (25, 26)
Yehoyakini anamasulidwa ku Babulo (27-30)