Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 9/8 tsamba 8-10
  • Chipembedzo mu Ndale Zadziko—Kodi Ichi Chiri Chifuno cha Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chipembedzo mu Ndale Zadziko—Kodi Ichi Chiri Chifuno cha Mulungu?
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Akazichita?
  • Kupereka Chiweruzo cha Mulungu
  • Kodi Mungakhale a Chete?
  • Kodi Zipembedzo Ziyenera Kuchita Nawo Zandale?
    Nkhani Zina
  • “Siali a Dziko Lapansi”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • “Siali a Dziko Lapansi”
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Salowerera Ndale?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 9/8 tsamba 8-10

Chipembedzo mu Ndale Zadziko—Kodi Ichi Chiri Chifuno cha Mulungu?

“ANAUKA YUDA wa ku Galileya, masiku akulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anawonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.” (Machitidwe 5:37) Pano tirinso ndi chitsanzo china cha mu Baibulo cha kusanganizana kwa chipembedzo mu ndale zadziko.

Mwamsanga Yesu asanabadwe, Yuda ameneyu ‘anandandalitsa chithandizo cha Asadoki, m’Farisi, ndipo anadziika iyemwini m’magwero a kuwukira.’ Ngakhale kuti Yuda “wansembe wokhala ndi kagulu ka iyemwini,” iye “anayesa kupangitsa afuko lake kuukira, akumanena kuti akakhala amantha ngati akanazigonjetsera ku kulipira msonkho kwa Aroma.”—Josephus’ The Jewish War.

Kodi Yesu Akazichita?

Mwamsanga pambuyo pa kubatizidwa kwa Yesu, Mdyerekezi anayesa kum’phatikiza iye mu ndale zadziko. Satana anampatsa iye “maufumu a dziko lonse ndi ulemerero wawo.” Kristu sanakane kuti Mdyerekezi anali ndi ulamuliro pa maboma. M’malo mwake, Yesu anakana mwaŵiwu wa ndale zadziko, ngakhale kuti akanalingalira kuti kukhala ndi mphamvu za ndale zadziko akakhala wokhoza kuchita zabwino kaamba ka anthu.—Mateyu 4:8-10.

Pambuyo pake anthu anawona kuyesayesa kwa Yesu kwakupereka zakudya. Iwo mwachiwonekere analingalira kuti, ‘chikanakhala kuti Yesu Kristu anali mu boma, iye akanakhoza kuthetsa mavuto athu a ndalama.’ Yang’anani chomwe chinatulukapo. “Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge mfumu, anachokanso.” (Yohane 6:10-15) Inde, Yesu anakana kulowetsedwa mu ndale zadziko, mosasamala kanthu za kuyenera kwake.

Pambuyo pakebe, Ayuda okhala ndi malingaliro a ndale zadziko anayesa kumtchera msampha Yesu pa nkhani ya ndale zadziko: misonkho. Kodi misonkho ya Chiroma inali yapamwamba kwenikweni? Ngati M’yuda analipira msonkho, kodi iye akasaina kugwiritsira ntchito msonkhowo kuchirikiza nkhondo ya Chiroma? Tingaphunzire chinachake kuchokera pa mmene Yesu anayankhira: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:13-17) Mosiyanako, abishopo a Chikatolika 225 mu United States anasankha November yapita kugwirizana ndi ndemanga ya zachuma yokhala ndi masamba 115 imene inati, mu mbali: “Dongosolo la misonkho lifunikira kukonzedwanso kuti lichepetse chotopetsa pa osauka. . . . Awo amene ali ndi zinthu zazikuluko mwachuma afunikira kulipira mlingo waukulu wa misonkho.”

Lingalirani chimene tingachite ponena za msonkho, Yesu anakhala chete ponena za misonkho ya ndale zadziko. Ophunzira ake, monga ngati mtumwi Paulo, anachita chimodzimodzi. (Aroma 13:1-7) Ngakhale pa nkhani ya mayanjano yovuta yonga ngati ukapolo, iwo anali achete. Inu mungalingalire mmene chikanakhalira chopepuka kwa Mkristu, motsogozedwa ndi chifundo, kuchita molimbana ndi ukapolo, ngakhale pamene atsogoleri achipembedzo tsopano akutenga mbali mu kuika mwalamulo kuchotsa mimba, tsankho la khungu, kuyenera kwa akazi, ndi zina zotero. Koma Akristu owona amakhala achete!

Profesa wa ku Oxford E. P. Sanders akulemba kuti: “Mwaubwino chiri tsopano chozindikiridwa mwa chilengedwe kuti palibiretu n’chidutswa chomwe chaumboni chimene chikatilola ife kuganiza kuti Yesu anali ndi malingaliro a magulu a nkhondo/malingaliro a ndale zadziko, ndipo chofananacho chimagwira ntchito kwa ophunzira ake.”

Kupereka Chiweruzo cha Mulungu

Monga mmene tawonera poyambapo, atsogoleri a Chiyuda ambiri anadzimva kuti chinali kaamba ka zikondwerero za ubwino wawo zimene iwo anadziphatikizira ndi olamulira a Chiroma, kuchita tero ngakhale pa kuyesedwa ndi kuphedwa kwa Yesu Mesiya. (Mateyu 27:1, 2, 15-31) Chivumbulutso chimawonetsanso kupanikiza kwa chipembedzo ndi kugwiritsira ntchito zinthu za ndale zadziko kukukhala monga ‘mkazi wakukhala pamwamba pa chirombo.’ Kodi icho sichimalingalira kwa inu mmene Mulungu amawonera kusanganizana kumeneku kwa atsogoleri achipembedzo?—Chivumbulutso 17:1-5.

Pano pali mmene ngakhale anthu openyerera akuweruzira nkhaniyo:

Malachi Martin, wophunzira wa Chivatican, anawona kuti akalaliki “omwe amatenga zochititsa ndale zadziko ndi mayanjano akulephera mu udindo wawo wa No. 1: Kukhala oimira a Yesu Kristu.” Iye anati: “Abishopo, mwachitsanzo, alibe kuyenera kwakulemba ponena za zachuma kapena kuuza prezidenti kusatumiza mamissile ku Europe.”

Koma kodi nchiyani chimene chidzachitika pamene a ndale zadziko ndi anthu atopa ndi kuchita malonda kwa ansembe? Chaka chatha magazini ya Liberty inakamba mmene Emperor Constantine mu zana lachinayi ‘anasanganizira ndale zadziko ndi chipembedzo, akumapanga chirombo cha “chipembedzo ndi boma”’ Iyo inati ponena za mkhalidwe lerolino: “Monga mmene zinaliri mu masiku a Constantine, tchalitchi chikugwiritsira ntchito boma kufikiritsa zifuno zake.”—Kanyenye ngwathu.

Mawu a Mulungu amachiwonetsera poyera mmene chotulukapo chake chidzakhalira. Nthaŵi irinkudza pamene zinthu za ndale zadziko zidzatembenuka ndi kuwononga ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, umene wakhala ukugwiritsira ntchito ndale zadziko ku mapeto ake Chivumbulutso 19:2 chimanena kuti uku kudzakhala kulongosola kwa chiweruzo cha Mulungu.

Kodi Mungakhale a Chete?

Inu mwaumwini simungaletse atsogoleri a chipembedzo kuchita malonda mu ndale zadziko. Koma panokha mungayese kumenyera kutsatira kulongosola kwa Baibulo ponena za wolambira wowona. Yesu ananena ponena za ophunzira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.” Pambuyo pake iye anauza woweruza Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda.”—Yohane 17:16; 18:36.

Kodi chiri chotheka mu nthaŵi yathu kukhala mu dziko, kukhala pa dziko lapansi monga nzika yalamulo ya mtundu wina, ndiponso “kusakhala mbali ya dziko,” kukhala wachete? Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova imayankha kuti inde. Iwo agwirizana ndi thayo la mu Baibulo lakukhala nzika zosunga lamulo, komabe kukhala achete kulinga ku ndale zadziko ndi machitachita a nkhondo a mitundu yambiri mu imene iwo akukhala.

Bukhu lakuti The Shaping of American Religion linati: “Mwakukana kuchita sawatcha ku mbendera kapena kutengamo mbali mu nkhondo zopanda cholinga za mitundu yowukiridwa, iwo kumbali ina ali nzika zosunga lamulo. Magulu ena ochepa athetsa mwaluso mavuto okhala ‘mu’ chitaganya chakunja mwakusakhalanso ‘a’ icho.” Ichi chakhala chowona dziko lonse lapansi mu mbali zonse za ndale zadziko. Ngakhale pansi pa chididikizo chokulira cha kuletsa uchete wawo, Mboni zapereka kudalira kwawo koyamba kwa Ufumu wa Mulungu.

Wodziŵa za mbiri yakale Brian Dunn akulemba kuti: “Mboni za Yehova zinali zosagwirizana ndi Chinazi . . . Ziletso zofunika za Nazi ku kaguluko zinali mkhalidwe wa Mboni kulinga ku boma ndi uchete wawo wa ndale zadziko. . . . Ichi chinatanthauza kuti kulibe mkhulupiriri aliyense akafunikira kunyamula chida cha nkhondo, kusankha, kulowa ntchito, kutenga mbali mu mapwando a poyera, kapena kusaina kuli konse kwa kulimbanira.”—The Churches’ Response to the Holocaust (1986).

Uchete woterowo wapitirizabe. Timaŵerenga mu The Modern Encyclopedia of Russian and Soviet History, voliyumu 15: “Hitler mwaukali anaphimba alambiri a Yehova ndi kuwaika mu ndende mwinamwake 10,000 a iwo . . . Mboni zolimbika mwa malingaliro zinalimbikira bwino lomwe mu ndende za chibalo za Chigerman kuposa aliyense . . . Boma la Chisoviet silinavomerezepo Mboni za Yehova kukhalapo mwalamulo, chifukwa chakuti limawona mu kaguluko, zambiri ngakhale kuposa zimene ziri mu kutembenuza kwa zipembedzo zina, lingaliro limene mwadala limagwetsa kugwirizana kwa chikhurupiriko ku boma. . . . Iwo samatenga mbali mu masankho; iwo amakana kutumikira mu magwero okhala ndi zida za nkhondo; amachepetsa kuziwonetsera kwawo ku kuulutsa kwa lamulo ku mlingo wochepetsa.”

Bukhu lakuti Christian Religion in the Soviet Union (1978) lawonjezera kuti: “Mboni za ku Soviet zimatsutsa kupanikiza kwa kutenga mbali mu kugwira ntchito kwa nkhondo, kusankha, ndi machitachita a ndale zadziko ena onse,” omwe amayembekezeredwa kwa nzika.

Chotero chiri chotheka kutsatira uchete wa Yesu ponena za ndale zadziko ndi zochitachita za magulu ankhondo a boma la Chiroma ndi Chiyuda. Kuchita tero lerolino kudzakhala chotetezera pamene Mulungu adzapereka chiweruzo chake chowopsya molimbana ndi kusanganizana kwa zipembedzo mu ndale zadziko.

[Bokosi patsamba 10]

“Iri nthaŵi ya kuchotsa ndale zadziko pa guwa ndipo guwa pa ndale zadziko. Adindo achipembedzo ali ndi kuyenera kuli konse kwa mawonedwe akunja aliwonse omwe ali nawo. [Koma] guwa likugwiritsiridwa ntchito molakwa pamene ligwiritsiridwa kaamba ka zochititsa zakunja.”—U.S. Assistant Secretary of State Langhorne Motley, June 1985.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena