Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 4-6
  • Umoyo Wabwino Kaamba ka Onse—Chofunika Chachikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Umoyo Wabwino Kaamba ka Onse—Chofunika Chachikulu
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto Amakono
  • Kusiyana m’Zathanzi kwa Padziko Lonse—Vuto Lomakula
    Galamukani!—1995
  • Umoyo Wabwino Kaamba ka Mtundu Wonse wa Anthu—Liti?
    Galamukani!—1987
  • Miliri m’Zaka za Zana la 20
    Galamukani!—1997
  • Bwanji Ponena za Umoyo Wabwino wa Inu Eni?
    Galamukani!—1987
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 4-6

Umoyo Wabwino Kaamba ka Onse—Chofunika Chachikulu

MANKHWALA amakono apanga kupita patsogolo kwapadera. Zifukwa za miliri yaikulu yakale sizikukhalanso za chinsinsi. Kupita patsogolo kodabwitsa kwatsogolera ku mankhwala ozizwitsa amakono.

Ngakhale kuli tero, mavuto aumoyo wabwino akhalabe odzandira. Pa nthaŵi ya msonkhano wa mu 1978 wa International Conference on Primary Health Care (Msonkhano wa Kusamalira kwa Umoyo m’Mbali za Kumidzi), maperesenti 80 a chiŵerengero cha anthu cha dziko m’mbali za kumidzi ndi m’matauni osauka chinasowabe njira yonkira ku ntchito iriyonse ya umoyo wabwino, ndipo 30 a ana 31 aliwonse okhala pansi pa msinkhu wa zaka zisanu omwe anafa chaka chimenecho anali omwe ankakhala m’maiko osauka kwenikweni. M’maiko “otukuka” kuipa kwa malo ozungulira, kuipitsidwa kwa mpweya, ndi zowonongedwa zovulaza zapitirizabe kupereka chiwopsyezo chomakulakula ku moyo.

Ofesi ya WHO ya dera la ku Europe siikuwoneratu umoyo podzafika chaka cha 2000 koma kuthekera kwa vuto kunthaŵiyo. Mu 1983 iyo inatulutsa bukhu lakuti, Health Crisis 2000, lolembedwa ndi Peter O’Neill, lomwe limalankhula ponena za “kuzindikira konthunthumira” kumene unyinji wa “matenda atsopano” alowelera nako mu dziko lamakono. Kodi amenewa nchiyani? Kansa yochititsidwa ndi malo otizinga, nthenda ya mtima, kumwerekera ndi anamgoneka, nthenda ya maganizo, matenda opatsirana mwa kugonana, “kusonkhezera kwa kudzipha, kwa wosuta ndi chidakwa,” ndi “‘mliri wa ngozi za pa msewu’, womwe walanda miyoyo ndi kuwumitsa zinthu zathu za chuma.” “Matenda a mu zitaganya zolemera” amenewa akufalikiranso ku mitundu yosauka kwenikweni.

Mavuto Amakono

Tiyeni tilingalire ena a mavuto a makonowa:

KANSA iri chochititsa imfa chapamwamba chachiŵiri mu United States. Iyo imapha munthu mmodzi pa anthu a ku Amerika anayi aliwonse. Kuzungulira dziko lonse, anthu mamiliyoni 40 angakhale akuvutika ndi nthenda imeneyi. Zinthu zodzetsa kansa zachuluka.

KUIPITSA. Zotulutsidwa zowopsya ndi zowonongedwa zovulaza zimaipitsa malo otizinga. Mankhwala ophera tizirombo amapezeka mu zakudya. Mitsinje ndi nyanja zaipitsidwa. M’malo ena ngakhale madzi a pansi pa nthaka omwe amatungidwa kuchokera mu zitsime amakhala oipitsidwa.

KUMWEREKERA NDI ANAMGONEKA. “Kutsetserekera ku imfa pang’onopang’ono” ndi chimene Health Crisis 2000 limatcha kumwerekera ndi anamgoneka. Ilo limati “njira yowonongera maganizo a wachichepere ndi thupi . . . iridi yochititsa mantha, ndipo njira yopulumutsira imatenga nthaŵi yaitali ndipo iri yovuta kwa wodwalayo ndi kwa awo omuthandizira, kotero kuti imafunikira kufufuza kwapadera.”

MATENDA OPATSIRANA MWA KUGONANA. Ndi kugwa kwa makhalidwe abwino, kufalikira kwa matenda opatsirana kwafikira mlingo pa umene kukutchedwa mliri—mliri wofalikira. Magazini ya World Health imati “kufalikira kwa nthendayi m’chiŵerengero cha anthu kwachititsidwa kukhala kofala lerolino kotero kuti munthu aliyense wa changu cha kugonana [mmodzi yemwe ali ndi ogonana nawo ambiri] ali pa ngozi yeniyeni ya kuyambukiridwa.”

KUGWIRITSIRA NTCHITO MOLAKWA ZAKUMWA ZOLEDZERETSA. M’malo ambiri akazi, oposa zaka khumi, ndipo ngakhale ana achichepere akukulitsa malo a anthu akumwa zakumwa zoledzeretsa. Zakumwa zoledzeretsa zanenedwa kukhala chochititsa cha 40 peresenti ya ngozi zonse za pamsewu. Ngakhale wakumwa kaamba ka masewera angawononge banja pamene akuyesa kutsimikizira kuyesayesa kwake pa kuyendetsa galimoto.

KUYENDA KWA MAKONO. Kupeputsa kwa kuyenda kwa makono kwapangitsa kukhala kothekera kufalikira kofulumira kwa mliri kuzungulira dziko lonse. AIDS ndi kuvuta kosamva mankhwala a penicillin kwa chindoko kwachititsidwa kufalikira kuzungulira dziko lonse ndi apaulendo, ndipo matendawa akunenedwa kukhala “atapeza mwaŵi wa kuyenda kokulira kwa chiŵerengero cha anthu komwe kwadziŵikitsa zaka za zana la makumi aŵiri.”

CHIŴERENGERO CHA ANTHU. Kukula koipa kwa chiŵerengero cha anthu ndi kusamuka kofulumira kwa chiŵerengero cha anthu okhala m’midzi kupita m’mizinda yodzaza kale ndi anthu kwawonjezeranso vuto la umoyo wa dziko. Mu 1983, mizinda 26 inali ndi chiŵerengero cha anthu cha chifupifupi mamiliyoni asanu. Podzafika chaka cha 2000 pangadzakhale mizinda 60 yoteroyo. Magazini ya World Health imati chotero pangadzakhale anthu oposa biliyoni imodzi “okhala m’mbali za ku matauni pa mlingo wosauka kowopsya.” Robert McNamara, prezidenti wakale wa World Bank, anachenjeza kuti: “Ngati mizinda sidzayamba kuchita ndi kusauka momangirira kwenikweni, kusaukako kungayambe kuchita movulaza kwenikweni ndi mizinda.”

Chotero, mosasamala kanthu za kuyesayesa kwa anthu ogwira ntchito mwakalavula gaga ndi odzipereka, cholinga cha “umoyo wabwino kaamba ka onse” chikuwonekera kukhala chosafikirika. Kunena zowona, kakambidweka sikafunikira kutengedwa m’chenicheni. Sikanalingaliridwe kutanthauza kuti aliyense akakhala waumoyo wabwino koma kuti kusamalira kwa umoyo m’mbali za kumidzi kudzakhalapo chifupifupi kwa onse. Cholinga, kabukhu ka WHO kanena kuti, chiri chakuti “chuma chaumoyo chidzagawiridwa bwino . . . ndikuti kusamalira kofunika ku umoyo wabwino kudzakhala kofikirika kwa aliyense . . . ndikuti anthu adzagwiritsira ntchito kufikira kwabwino kuposa ndi mmene akuchitira tsopano” pa kuchinjiriza ndi kuchotsapo matenda ndi kupunduka.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

P. Almasy/WHO

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena