Kuchiritsa Kosatha Kuli Pafupi
SAYANSI ya za mankhwala, ndi kupita kwake patsogolo kozizwitsa, kungapambane kumenyanako—koma imalepherabe nkhondo. Pamene tidzimvera kuti ife takulitsa maluso ndi kuyeneretsedwa, ukalamba umayamba kutibweza m’mbuyo, ndipo imfa imabwera mwamsanga. Komabe Mulungu amalonjeza kuti sichidzakhala nthaŵi zonse mu njira yoteroyo. Kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, Mulungu ananena kuti iye ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndi kupukuta misozi pa nkhope zonse.’—Yesaya 25:8.
Kodi chimenecho chimamvekera kukhala chovuta kukhulupirira? Kodi mumalingalira kuti umoyo wa zaka 80 uli nthaŵi yaitali? Pali mitengo imene imakhalapo kwa zaka zikwi zingapo—nchifukwa ninji inu simungatero? Mulungu anapatsa starfish mphamvu za kukulitsanso mkono watsopano wathunthu pamene wina waduka. Kodi iye sangabwezenso thupi lanu ku umoyo wangwiro ndi wathunthu?
Chifupifupi zaka 2,000 zapita Yesu Kristu anachita zozizwitsa zodabwitsa padziko lapansi. Iye anachiritsa osati kokha khate koma “nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.” Mawu ouziridwa amanena kuti iye anachiritsa “anthu opunduka miyendo, akhungu, osalankhula . . . Kotero kuti khamulo linazizwa, pa kupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya.” Yesu sanafune osonkha minofu kapena kusamutsa ziwalo—iye anachiritsa ziwalo zenizenizo kapena mbali zathupi zomwe zinali zodwala. Ndipo anazichiritsa pomwepo, nthaŵi zina ngakhale kuchokera ku malo akutali.a
Osati kokha kuti Yesu Kristu anali ndi mphamvu za kuchiritsa koma analinso ndi kufunitsitsa kwa kuchita tero. Pa nthaŵi imodzi, wakhate anati kwa iye: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Yesu, mogwidwa ndi chifundo, anamkhudza iye nanena kuti: “Ndifuna; khala wokonzedwa.” Iye anaukitsanso ngakhale akufa—pachochitika chimodzi ngakhale pambuyo pakuti kuwola kwathupi kunali kutayambika.—Marko 1:40-42; Yohane 11:38-44.
Kodi zitsanzo zozizwitsazi zimasonyezanji? Kuti Yesu, amene tsopano waikidwa monga Mfumu ya kumwamba, sali kokha ndi mphamvu komanso ndi kufunitsitsa kubweretsa kuchiritsa kwenikweni ndi kosatha. Iye adzachita monga mmene Baibulo limalonjezera.
Bukhu limenelo, Baibulo, limalongosola kusintha kozizwitsa kumene kudzabwera posachedwapa mu zochitika za anthu—kulowerera kwa Mulungu iyemwini mu zochita zadziko ndi kukhazikitsanso kwadziko lapansi laparadaiso lopanda kuipitsidwa kwa mpweya, kudwala, upandu, kuipa, ndi nkhondo. Ilo limanena ponena za kuchiritsa kwenikweni ndi kosatha, ponse paŵiri kwa kuuzimu ndi kwa kuthupi. Ndipo maulosi a Baibulo amasonyeza kuti panali anthu omwe analipo kumbuyoku mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya I omwe adzakhalapo ndi moyo pamene kusintha kwadziko lonse kuyamba kuchitika.—Mateyu 24:3, 14, 34.
Umoyo Wowona
Mitu yotsekera ya Baibulo imanena ponena za kulamulira kolungama komwe kukudza “kuchokera kumwamba kwa Mulungu”—ku mtundu wa anthu padziko lino lapansi. Ndiyeno Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira kapena chowaŵitsa. Zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:2-4) M’lingaliro lenileni ndiponso ndi lauzimu, “maso a akhungu adzatsegulidwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.” “Ndipo okhalamo sadzanena: ‘Ine ndidwala.’”—Yesaya 35:5, 6; 33:24.
Chotero, osati kokha chithandizo cha zamankhwala ndi kuchiritsa kwanthaŵi yochepa, koma kuchiritsa kwenikweni kaamba ka onse kuli lonjezo kwa awo omwe adzakhala pansi pa Ufumu wa Mulungu padziko lino lapansi. Ndithudi ilo liri chonulirapo chonunkha kanthu pa chimene tifunikira kumenyera!
[Mawu a M’munsi]
a Inu mungaŵerenge zolembedwa zodalirika za zochitikazi m’mbali zotsatirazi za Baibulo: Mateyu 4:23; 15:21-31; Marko 5:25-34; 7:31-37; Luka 7:1-10; 13:11-13; Yohane 9:1-32.