Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 10-13
  • Ndiri Woyamikira ndi Zimene Ndiri Nazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndiri Woyamikira ndi Zimene Ndiri Nazo
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi Chigonjetsa Kusowa Chithandizo
  • Thandizo Lachikondi
  • Chithandizo M’kugonjetsa Kusowa
  • Zambiri Zoyamikirira
  • Yehova Wandipatsa Nyonga
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Ndidzadumpha Ngati Nswala’
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 10-13

Ndiri Woyamikira ndi Zimene Ndiri Nazo

Kodi munthu amachita bwanji pamene tsoka lakantha ndi kumusiya iye wopanda chochita? Kodi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu ndi malonjezo ake chimapanga kusiyana? Kodi banja lidzayankha motani? Kodi chiri chotheka kwa onse kusungilira kawonedwe kenikeni? Yotsatira iri nkhani ya kulimbikira kwa banja lina kuchita nazo.

JUNE 1, 1957, linali tsiku lomalizira “labwino” la umoyo wanga. Ilo linayamba monga mmene masiku ena onse amayambira: Ndinauka m’mamawa ndi kupita ku ntchito yanga monga wodula mitengo mu Deer Lake, Newfoundland. Zonse zinawonekera bwino.

Mwadzidzidzi, mtengo waukulu umene ndinali nditangodula, ndipo umene unali pa ulendo wake wodzagwera pansi, unagwidwa ndi mphepo imene mosayembekezereka inautembenuza iwo kukagwera kumbali ina! Kunali kuchedwa kwenikweni kwa ine kuchoka pamalowo. Mtengowo unadzamenya pansi pamapewa anga, kundigwetsa ine pansi ndi kundisiya wokomoka. Pambuyo pake, pamene ndinauka, sindinakhoze kuyenda!

Ndinatengedwa ku chipatala mu Corner Brook. Mayeso akuya anavumbula kuti nkolofupa wanga wa ku msana unavulazidwa pang’ono, chakuti kunafunikira kuchotsa mafupa aŵiri a ku msana. Ndinasiyidwa ndi ziwalo zakufa kuchokera kukhosi kufikira pansi!

Chikondi Chigonjetsa Kusowa Chithandizo

Chiri chovuta kulingalira mmene kusowa chithandizo kotheratu ndi kuvutitsidwa kumene tsoka loterolo lingabweretse. Sindinali wokhoza ngakhale kupesa tsitsi langa kapena kuzidyetsa inemwini. M’chenicheni, sindinakhoze ngakhale kunena pamene ndinali ndi njala!

Ndinali munthu wamkulu, wolimba ndi wamphamvu. Tsopano ndinachepetsedwa kukhala munthu wopunduka wopanda chithandizo. Chotero masinthidwe ambiri anafunikira kuti ndikhale wokhoza kuchita ndi umoyo. Kodi munthu akakhoza kuchita mochulukira motani? Ndinayenera kuzipeza mu zaka zambiri zomwe zikatsatira.

Sindikanakhoza kuchita nazo popanda kusamalira kwachikondi kwa mkazi wanga Hilda. Baibulo, pa Miyambo 18:22 [NW], limafunsa kuti: “Kodi wina wapeza mkazi wabwino?” Ngati ndi tero, ilo limanena kuti “wapeza chinthu chabwino.” Zowonadi mkazi wanga anali dalitso kwa ine ndi kwa banja lathu la ana asanu ndi aŵiri.

Wochepetsetsa wa ana athu anali wa miyezi 18 pa nthaŵi ya ngozi yanga, chotero kufikira panthaŵiyo nthaŵi yochulukira ya Hilda yakhala ikuwonongedwa kaamba ka kuwasamalira. Kenaka ndinadzakhala monga mmodzi wa iwo, ndipo ngakhale kuposerapo, popeza kuti sindinakhoze kuikidwa pansi kuyendayenda ndi kusewera pambuyo pa kusambitsidwa ndi kuvekedwa. Ayi, ndinafunikira kunyamulidwa ndi kuikidwa pa kama.

Ndiponso, panali nthaŵi zina pamene tinapeza zinthu kukhala zoseketsa. Mwachitsanzo, mkazi wanga anali kundichotsa kaŵirikaŵiri pa mpando wanga wa magudumu. Pa nthaŵi ina ndinapitirizabe kugwera kumbali ina ya mpando wa magudumu. Iye ankakhoza kundinyamula ndi kundiimitsa, koma chinawonekera kuti sindinali wokhoza kuimitsidwa tsiku limenelo. Hilda potsirizira pake ananena kuti: “Lindsay, kodi chavuta nchiyani?” Tinakapeza pamene tinafika kunyumba. Pamene iye anandichotsa pampando wanga, panali chitini chachikulu chapaudala chomwe chinali pomwe ndinali khale! Popeza kuti kumvera kunali kunatha, sindinadziŵe chirichonse ponena za icho. Chotero ndi kulemera kwanga kosalinganizidwa bwino, ndinapitiriza kupendekera ku mbali imodzi.

Thandizo Lachikondi

Mosasamala kanthu za mkhalidwe wanga wovuta, chikondi cha Yehova Mulungu chandisungilira ine. Miyambo 3:5, 6 imatilangiza ife ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe athu.’ Mmene chiriri dalitso chimenecho, popeza kuti ngati sichikanakhala chikondi cha Yehova ndi chowonadi cha Baibulo, sindikanakhala wokhoza kupirira. Koma sindinakhale wokhulupirira Yehova nthaŵi zonse. M’chenicheni, panali nthaŵi ina pamene sindinamudziŵe nkomwe.

Ndinabadwa mu 1911 pa malo otchedwa Little Catalina, Trinity Bay, Newfoundland. Ndinaleredwa ndi makolo achipembedzo, ndinalilemekeza Baibulo ndipo ndinaliŵerenga ilo kamodzikamodzi. Pamene ndinachita tero, mafunso anabwera ku malingaliro anga, onga ngati: Kodi munthu ndithudi angakhale kosatha padziko lapansi, monga mmene Masalmo 37:29 imanenera? Kuti ndipeze yankho, ndinapita kwa mkulu wanga wa chipembedzo ndi kumufunsa. Yankho lake linali lakuti: “Udzafunikira kuyembekeza kufikira ‘utawoloka Yordano’ kuti upeze.” Mafunso ambiri kuchokera kwa ine anawonekera kukhala akumsokoneza iye. Chotero iye anati kwa ine: “Vuto lako, Lindsay, liri lakuti iwe umafunsa mafunso ambiri.”

Sindinapeze yankho kufikira mu 1948 pamene tinasamukira ku mudzi wa Cormack. Kumeneko ndinakumana ndi Gus Barnes ndi Jack Keats, amene anali Mboni za Yehova. Mmene ndinaliri wokondwera pamene amunawa anandisonyeza mayankho kuchokera mu Baibulo! Ndinali wokondweretsedwa chakuti chaka chotsatira ndinabatizidwa m’chisonyezero cha kudzipereka kwanga kwa Yehova.

Chaka chimodzimodzicho tinasamukanso, panthaŵiyi cha kumpoto ku Goose Bay, Labrador, kumene ndinafunikira kugwira ntchito ndi chiwiya chachikulu. Sipanapite nthaŵi pamene wondilemba ntchito wanga anapeza kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova. Mkati mwa miyezi iŵiri ndinachotsedwa ntchito ndipo ndinauzidwa kuchoka m’mzindawo. Ndinakana kuchita chimenechi. M’masikuwo anthu anali amantha kumvetsera ku chinthu china chake chatsopano, ngakhale kuti uthenga umenewu unali wakale kwambiri kuposa ndi mmene iwo analiri.

Ana anga sanapite popanda kudziwidwa. Iwo anapatsidwa nthaŵi yovuta pa sukulu mpaka apolisi anapita ku maulamuliro a sukulu ndi kuwakumbutsa iwo kuti Mboni za Yehova zinamenyera ndi kupambana milandu yomveka yambiri ya m’mabwalo a milandu mu Canada pa nkhani ya ufulu wa chipembedzo. Chotulukapo chinali chakuti ana anga, ndi ana azipembedzo zina, anatsimikizidwa ponena za ufulu wa chipembedzo chawo.

Zinthu ziri zosiyana m’malo amenewo lerolino. Mu 1985 Nyumba ya Ufumu yomangidwa mofulumira inamangidwa ndi mpingo wa anthu a Mboni za Yehova olimbikira amene anaphatikizapo m’modzi wa ana anga akazi.

Chithandizo M’kugonjetsa Kusowa

Mu 1951 tinasamukira ku mzinda kumene tikukhala mpaka pano, Deer Lake. Chipiriro chinali chofunika pa zaka za mavuto zonsezo. Koma zinthu zinali kubwera zimene zikaitainira ngakhale kaamba ka chipiriro chokulira.

Mkazi wanga wokondedwa kwanthaŵi yaitali, Hilda, yemwe anali ndi vuto la mtima, anamwalira kaamba ka kukanthidwa mu 1963. Patsiku lozizira la nyengo ya chisanu, pamene ndinali kupenyerera pa mpando wanga wa magudumu, iye anaikidwa m’manda. Kusungulumwa kumene ndinamvera kunawoneka kukhala kosapiririka! Kodi nchiyani chimene ndikachita tsopano? Ndinali wosakhoza kotheratu kudzisamalira ine mwini, ndipo osatchulanso kusamalira banja langa.

Koma Yehova ali wokhulupirika, ndipo nthaŵi zonse amapanga njira yotulukira kaamba ka ife ngati tidalira pa iye. (1 Akorinto 10:13) Atumiki ake, abale anga Achikristu ndi alongo, anandipatsa ine chitonthozo chochulukira, chimene chinandilimbikitsa ine kupitirizabe. Mwana wanga wamkazi Yvonne anaitenga ntchito ya kundisamalira. Ndi dalitso lotani nanga limene iye watsimikizira kukhala!

Ngakhale kuti Yvonne ali ndi banja lofunikira kusamalira la iyemwini, iye wapitirizabe kuwona kusoweka kwanga. Chipatala chimene chiri pafupi chiri pa mtunda wa mamailosi 30 (50 km). Nthaŵi zambiri mwana wanga wamkazi anafunikira kunditenga ine kumeneko kaamba ka kupatsidwa mankhwala. Pamene vuto laumoyo wanga lakhala lowopsya, ndimapanga ulendo ndi ndege ku chipatala chimene chiri mu St. John’s, chifupifupi mtunda wa mamailosi 400 (640 km). Yvonne nthaŵi zonse amandiperekeza.

Chifukwa cha kusowa mphamvu ya kugwira ntchito kwa thupi langa monga mmene lifunikira, kudwala kowopsya kumandipambana ine nthaŵi zina. Ndakhala nditachotsedwapo miyala mu imso; kuyambukiridwa kumene kaŵirikaŵiri kumafunikira kutumbulidwa; zironda zowawa zandipangitsa ine kukhala m’chipatala kwa miyezi ingapo ndipo kukhala mu kama kunyumba kwa miyezi yowonjezerapo, zina za zironda zimenezi zofunikira kusamalira kwa luso; mavuto a m’mimba atsogolera ku kutumbulidwa kwa matumbo a akulu; ndipo nthenda ya shuga nayonso inabwera mu kawonedwe.

Nkhani ponena za kupatsidwa kwa mwazi zinauka kaŵirikaŵiri. Koma potsirizira pake adokotala anavomereza kunditumbula ine popanda mwazi. Kaamba ka luso lawo ndi kudera nkhaŵa, ndinatuluka bwino lomwe popanda kupatsidwa mwazi.—Machitidwe 15:29.

Mwana wanga wamkazi ndi mwamuna wake ndi banja andiwona ine kupyola m’mavuto anga onse, kuwuka usiku kuti andisamalire ine, kundidyetsa, kundisambitsa, kusintha nsalu za pachironda zanga, kunditenga ine ku misonkhano Yachikristu ndi misonkhano yaikulu, kumene kachiŵirinso ndimalimbikitsidwa mwauzimu. Panthaŵi zina ndimatengamo mbali mu programu ya msonkhano. Ana achikondi ndithudi ali dalitso lochokera kwa Yehova!—Masalmo 127:3.

Zambiri Zoyamikirira

Inde, ndiri ndi zambiri zofunikira kuyamikira. Pamene kuli kwakuti umoyo wanga wakuthupi uli wosakhoza kugwira ntchito, bongo langa liri logalamuka, ndipo ndingakhoze kulankhula. Ndagwiritsira ntchito kuyesayesa kumeneku kudziŵikitsa dzina la Yehova ndi zifuno zake kwa awo okhala mu chipatala omwe angakhoze kumvetsera—adokotala, anamwino, odwala, akulu azipembedzo omwe amachezera zipatala, ndi mabwenzi omwe amadza kudzandiwona.

Kuwonjezerapo, ndatsiriza maphunziro a mpando wa magundumu woyendetsedwa ndi mphamvu za magetsi 12 za mabatiri, womwe ndimayendetsa ndi choyatsira chomwe chiri poika dzanja. Panthaŵi zina pamene ndiri kunja m’mpando wanga, ndimakumana ndi mabwenzi ndi achinansi ndipo ndimakhala ndi mwaŵi wowonjezereka, wa kulankhula kwa iwo ponena za zifuno za Mulungu. Ndiri woyamikira kuti ndiri wokhoza kuchita tero.

Ambiri a ana anga apereka miyoyo yawo kwa Yehova, ndipo iwo monga chotulukapo akuphunzitsa ana awo kutumikira Mulungu. Chimenechi chimandidzetsera ine chisangalalo chachikulu. Mkazi wanga anali wolambira wobatizidwa wa Yehova, ndipo amayi anga, omwe anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 75, anatumikira Yehova kufikira imfa yawo.

Tsopano ndikuyang’ana kutsogolo ku tsiku pamene ‘Mulungu iyemwini adzakhala ndi anthu ake ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo pamene imfa sidzakhalako, ngakhale kulira kapena kufuula kapena chowaŵitsa chirichonse,’ ndipo pamene “wopunduka adzatumpha ngati nswala.”—Chivumbulutso 21:3, 4, NW; Yesaya 35:5, 6.

Panthaŵi imeneyo mtendere wochuluka udzadzaza dziko lapansi, ndipo awo ogonjera ku lamulo la Mulungu adzapeza madalitso. Baibulo limalonjeza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Kwa utali wotani? “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Masalmo 37:11, 29; 72:7.

Izo ziri zinthu zodabwitsa zomwe tiyenera kuyembekezera kutsogolo. Ndipo chisangalalo changa chidzakhala chokulira pamene, m’dongosolo latsopano la Yehova, ngakhale ‘ali m’manda adzatulukira.’—Yohane 5:28, 29.

Pamene ndigona pano tsiku ndi tsiku, ndimakhala ndi mwaŵi wa kubwereramo mu umoyo wanga ndi kuwona ngati ndapindula mu njira iriyonse. Ndinganene popanda kusinkhasinkha kuli konse kuti ndapindula koposa. Uzimu wanga wawonjezereka mokulira. Ndaphunzira kudalira pa Yehova kwakukulukulu. M’malo modandaula ponena za zambiri mu umoyo wanga kapena chimene ndikusowa, ndaphunzira kuyamikira chimene ndiri nacho. Ndipo kuyamikira kwanga kaamba ka banja langa lachikondi ndithudi kwakula.

Chotero ndiridi woyamikira kaamba ka zimene ndiri nazo tsopano, ndipo ndiyang’ana kutsogolo kukukwaniritsidwa kwa lonjezo lodabwitsa limene liri kutsogolo—moyo mu dongosolo latsopano la Mulungu. Ndiyeno ndidzakhala ndi umoyo wangwiro. Lidzakhala tsiku lachimwemwe chotani nanga limenelo!—Monga Momwe kwasimbidwira ndi Lindsay Stead.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Imfa ya mkazi wanga wokondedwa inaitanira ngakhale kaamba ka chipiriro chokulira

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Ana achikondi ndithudi ali dalitso lochokera kwa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena