Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 2/8 tsamba 13-15
  • Chiyembekezo Kaamba ka Akufa, Chitonthozo kwa Okhala ndi Chisoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiyembekezo Kaamba ka Akufa, Chitonthozo kwa Okhala ndi Chisoni
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyembekezo kaamba ka Akufa—Monga Momwe Yesu Anaphunzitsira
  • “Lemba Langa Lapamtima Liri . . . ”
  • Chiyembekezo kaamba ka Akufa—Chidzakhala Chenicheni Posachedwapa
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Njira Yokhayo Yothetsera Imfa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Akufa Adzaukitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 2/8 tsamba 13-15

Chiyembekezo Kaamba ka Akufa, Chitonthozo kwa Okhala ndi Chisoni

JESS Romero, wotchulidwa m’nkhani yathu yotsegulira, potsirizira pake anakwatiranso. Ponena za Agustín ndi Valentina Caraballoso, kwa iwo imfa ya Jonathan ikali kuvutabe, koma bata langoyambitsidwa. Ramón ndi María Serrano a ku Spain amapitirizabe kulira zaka 24 pambuyo pa imfa ya Paquito. Komabe m’nkhani zonsezi, kodi nchiyani chimene chawasunga iwo kupitirizabe? Iwo akuyankha: “Chiyembekezo kaamba ka kuukitsidwa!”

Komabe nchiyani chimene timatanthauza kwenikweni mwa “kuukitsidwa”? Kodi ndani omwe adzaukitsidwa? Liti? Ndipo ndimotani mmene tingakhalire otsimikizira?

Chiyembekezo kaamba ka Akufa—Monga Momwe Yesu Anaphunzitsira

Mkati mwa utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anaukitsa anthu osiyanasiyana. (Marko 5:35-42) Ichi chinatumikira monga chitsanzo cha kuukitsidwa kwakukulu komwe kudzachitika pamene dziko lapansi kachiŵirinso lidzakhala pansi pa ulamuliro wa Mulungu kotheratu, monga momwe mamiliyoni ambiri amafunsira pamene apemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Chitsanzo cha mphamvu ya Mulungu m’nkhaniyi chinali pamene Yesu anaukitsa bwenzi lake Lazaro. Panthaŵi imodzimodziyo, cholembedwa chimawunikira mkhalidwe wa akufa. Yesu ananena kwa ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” Pambuyo pa kulephera kupeza tanthauzo lake, ophunzira ananena kuti: “Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira.” Iwo analingalira kuti iye anali kunena kuti Lazaro anali kokha gone pamene, m’chenicheni, iye anali atafa. Chotero, Yesu sanasiye mbali iriyonse kaamba ka kukaikira: “Lazaro wamwalira.”

Dziwani, chonde, kuti Yesu sanapange chilozero chirichonse ku moyo wosafa wosinthidwira ku mkhalidwe wina wa ufumu. Iye sanayambukiridwe ndi nthanthi ya Chigriki koma ndi chiphunzitso chomvekera bwino cha Baibulo m’malemba Achihebri. Lazaro anali gone mu imfa ndipo pamene Yesu anafika iye anali atatha masiku anayi m’manda a chikumbukiro. Chotero, kodi ndi chiyembekezo chotani chomwe chinalipo kaamba ka iye?

Pamene Yesu analankhula kwa mlongo wa Lazaro Marita, iye anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Kodi iye anayankha motani? Kodi iye ananena kuti moyo wake unali kale m’mwamba kapena kwinakwake? Kuyankha kwake kunali kwakuti: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” Iye anakhaliriranso ku chiphunzitso cha Baibulo cha kuukitsidwa ku moyo padziko lapansi. Yesu anampatsa iye ngakhale kulingalirapo kokulira kwa chikhulupiriro mwakunena kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, ngakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” Kenaka, kutsimikizira nsonga yake, iye anapita ku manda a Lazaro ndi kufuula ndi mawu akulu: “Lazaro, tuluka!” Kodi chinachitika nchiyani?

Nkhani ya m’mbiri imanena kuti: “Womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nawo, ‘Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.’”—Yohane 11:1-44.

Mmenemo muli chiyembekezo chomwe chathandiza anthu oferedwa ambiri ofunsidwa ndi Galamukani! Chiyembekezo chimodzimodzicho chinawasungirira iwo kuyang’ana kutsogolo posachedwa pamene dziko lapansi lidzapangidwanso paradaiso ndipo pamene mawu ouziridwa a Yesu adzakwaniritsidwa: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruzidwa.”—Yohane 5:28, 29.

“Lemba Langa Lapamtima Liri . . . ”

Galamukani! yafunsa makolo ndi achichepere ponena za imfa ya mwana m’banja.a Nthaŵi ndi nthaŵi, polongosola mmene achitira ndi kumva chisoni kwawo, iwo anena kuti: “Ndiloleni ndikuuzeni lemba langa la pamtima.” Ngati inu muli ndi chisoni, mwinamwake malemba amenewa adzakuthandizaninso.

Yunhee wa zaka za kubadwa khumi ndi zinayi, kuchokera ku Seoul, Republic of Korea, anafa ndi nthenda ya kuchepa kwa mwazi mu 1985. Atate wake, Chun Kwang-kook, analongosola kwa Galamukani! mmene iye anatonthozera Yunhee m’milungu yothera ya umoyo wake: “Ndinamuuza iye ponena za Lazaro. Yesu ananena kuti Lazaro anali gone, ndipo ponena za iye, pamene Yesu adzaitana kuti, ‘Yunhee! Tauka!’ iye nayenso adzuka kuchokera kutulo.”

Janet Hercock, kuchokera ku England, anali wa zaka 13 pamene anafa ndi kansa mu 1966. Iye anasiya makolo ake ndi abale aŵiri, David ndi Timothy. David anauza Galamukani! lemba limene linali lathandizo kwambiri kwa iye: “Ilo linali Machitidwe 17:31, limene limanena kuti: ‘Chifukwa [Mulungu] anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu, napatsa anthu onse chitsimikiziro, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.’ Pa maliro, mlankhuli anagogomezera kuti kuukitsidwa kwa Yesu kuli chitsimikiziro chathu cha chiukiriro chamtsogolo. Chimenecho chakhala maziko a akulu achilimbikitso kwa ine.”

Mu December 1975 George wachichepere, kokha wa zaka za kubadwa 14, anatenga mfuti ya atate wake ndi kudzilizira iyemwini. Kodi ndimotani mmene atate wa George, Russell, anachitira ndi kutaikiridwa kwa kudzipha kwa mwana wake kumeneku?b

“Malemba ena anakhala chochirikiza kwa ine. Mwachitsanzo, mawu a Miyambo 3:5: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.’ Kumlingo winawake ndinali kuyedzamira pa luntha langa mkuyesa kudzigwirizanitsa inemwini ndi chimene chinachitika.”

Banja la a Morgan kuchokera ku England, linali mu Sweden pamene mwana wawo wamwamuna Darrall anadwala mwadzidzidzi. Kutumbulidwa kwa mwamsanga kunachitika mu Stockholm. Potsirizira pake, iye anatengedwa pa ndege kubwerera ku England, kumene iye anafa mwamsanga lisanafike tsiku lake la kukwanitsa zaka za kubadwa 24. Amayi wake Nell akunena kuti: “Lemba limodzi lomwe limaima m’malingaliro anga liri Mateyu 22:32, pamene Yesu anagwira mawu Mulungu monga akunena kuti: ‘Ine ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.’ Kenaka anapitiriza kuti: ‘Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo.’ Ndimadziŵa kuti mawu amenewo amatanthauza kuti Darrall akukumbukiridwa ndi Mulungu ndipo adzabwera m’chiukiriro.”

Chiyembekezo kaamba ka Akufa—Chidzakhala Chenicheni Posachedwapa

Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti tiri pafupi ndi nthaŵi pamene Mulungu adzagwira ntchito kubwezeretsa mtendere ndi moyo wosatha ku mtundu wa anthu omvera. Mulungu amalonjeza kuti: “Pakuti ndidzasandutsa kulira kwawo kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yawo, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chawo.” “‘Letsa mawu ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphoto,’ ati Yehova; ‘ndipo adzabweranso kuchokera ku dziko la mdani [imfa].’”—Yeremiya 31:13-17.

Panthaŵi imeneyo Yehova adzabwezeretsa mopita patsogolo ku moyo kudzera m’kuukitsa aja omwe anafa kupyola m’mbiri ya munthu. Pansi pa boma la kumwamba la dongosolo latsopano la Mulungu, iwo adzakhala ndi mwaŵi wa kusankha moyo wosatha mwa kumvera ku malamulo a Mulungu kaamba ka moyo panthaŵiyo. Chotero, ngati titembenukira ku Baibulo, tidzapeza kuti pali chiyembekezo chowona kaamba ka akufa ndi chitonthozo kaamba ka amoyo.—Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 20:12-14; 21:1-4.

[Mawu a M’munsi]

a Kope la kutsogolo la Galamukani! lidzalingalira kuyankha kwa mwana ku kutaikiridwa kwa mbale kapena mlongo.

b Nkhani ya kudzipha ndi kumva chisoni kwa makolo idzakwaniritsidwa m’kope lamtsogolo la Galamukani!

[Bokosi patsamba 14]

Diane Krych, yemwe walongosola imfa ya mwana wake David m’nkhani yathu yachiŵiri, anapyola m’kumva chisoni kwakukulu ndi ziyambukiro za kukana. Ichi chinawonedwa ndi makalata omwe iye analemba kwa David, ndi kupitirizabe, kwa zaka 13. Iye analeka kulemba pamene anayang’anizana ndi zenizeni za imfa ya atate wake, omwe iye analera. (Galamukani! sikuyamikira kulemba makalata monga chothetsa chisoni. Komabe, tikugwira mawu a kalata yoyambirira kuchitira chitsanzo mmene chiyembekezo cha chiukiriro chinaliri chirikizo lake lalikulu ndi mmene chamuchirikizira iye chiyambire pamenepo.)

Wokondedwa David,

Wakhala ukugona kwa masiku 46 tsopano. Chikuwonekera kukhala monga zaka chiyambire pamene ndinakuwona iwe ndi kukusunga. Koma masiku kaamba ka kugona kwako ali ndi porekezera. Ndikungokhumba kuti ndidadziŵa chiŵerengero chake chifukwa ndikadapitiriza kuchotsapo tsiku limodzi ndi limodzi pa masikuwo. Kwa ife, chiri nthaŵi yaitali, yovuta, kuyembekeza kosungulumwa, koma kwa iwe chidzawonekera monga mphindi zoŵerengeka. Ndiri woyamikira kaamba ka chimenecho. Tikuyang’ana kutsogolo ku tsiku pamene Yehova adzakuukitsa iwe kuchoka ku kugona kwako m’dongosolo latsopano. Tidzakhala ndi phwando lalikulu lomwe sunawonepo. Ilo lidzatenga chifupifupi masiku atatu. Aliyense amene timadziŵa adzaitanidwa. Lidzakhala phwando lako. Ndingokhumba kuti sitidzayembekezera kwa nthaŵi yaitali. Sindingayembekeze kukufungata iwe m’manja anga, David. Tonsefe tikukusowa iwe mokulira. Nyumba iri yopanda kanthu popanda iwe. Palibe chirichonse chimene chidzakhala chofanana kufikira utabwera kunyumba kudzakhala ndi ife.

Chotero, mwana wanga wokondedwa, tidzayesa kukhala oleza mtima ndi kuyembekeza pa Yehova kaamba ka kubwera kwako, ndipo pa nthaŵi ino, tidzakulembera makalata oŵerengeka kukudzadza iwe pa chimene chingachitike pamene uli gone.

Ndi chikondi changa chonse,

Mayi wako

[Zithunzi patsamba 15]

Baibulo limalonjeza kuti akufa, onga ngati Maria ndi David, adzaukitsidwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena