Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 3/8 tsamba 27-30
  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Wokonzanso Watsopano Angathandize?
  • Ngati Tchalitchi Chanu Chilephera Kuchitapo Kanthu, Kodi Mudzatero Nanunso?
  • Kodi ma Lutheran AchiGerman ali Mtundu Wowopsyezedwa?
    Galamukani!—1988
  • Carici Coona ndi Maziko Ace
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • “Ngati Lipenga Lipereka Mawu Osazindikirika . . . ”
    Galamukani!—1988
  • Kulepa Zochuluka Chifukwa cha Kanthu Kena Kokulirapo
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 3/8 tsamba 27-30

Ziyembekezo za Mtsogolo Kaamba ka chiProtestanti—Ndi Inu!

“NDAKHALA ndikuphunzira maphunziro a zaumulungu a Lutheran tsopano kwa nyengo zisanu ndi ziŵiri ndipo chotero ndine m’minisitala woyembekezeredwa wa tchalitchi.” Inayamba tero kalata yonka kwa mkonzi wa nyuzipepala ya chiGerman ya pa November 1986. Iyo inapitiriza kuti: “Ndingakonde kuitanira chisamaliro ku nsonga yakuti kuphunzitsidwa kwathu kuli kodzala kwakukulukulu ndi kukhadzula Baibulo pakati—kokha zikuto zake zimatsala. . . . Pamene chikhulupiriro cha wophunzira kapena maziko ake, Malemba, zikuwonongedwa, ambiri a aphunzitsi akumuphunzitsa iye ‘uthenga watsopano’ wa chisosholizimu, chotero kupereka ku tchalitchi kalongosoledwe katsopano kotheratu. Mulungu ali wakufa—chikhale kwa nthaŵi yaitali chisosholizimu! Yesu waola m’manda ake, tiyenera kudzipulumutsa ife eni! Uwu ndi uthenga umene aminisitala ambiri amatenga ku guwa lawo, Sande iriyonse. Ife mofulumira tifunikira ziwiya zatsopano kuti zitiphunzitse ife Baibulo, koma pakali pano chipembedzo chikuzididikiza izo.”

Ndi Mawu a Mulungu kukhala akuchitidwa moipa chotero, kodi pali chiyembekezo chirichonse chakuti tchalitchi ndi ochitsogolera ake chingachire kuchoka ku matenda ake auzimu? Wotembenuza Baibulo wa m’zana la 18 anawona molondola kuti: “Mkhalidwe wa umoyo wa tchalitchi umalingaliridwa ndi njira mu imene chimachitira ndi Malemba.”

Kodi Wokonzanso Watsopano Angathandize?

“Dietrich Bonhoeffer akulemekezedwa ndi kugwidwa mawu lerolino kuposa wophunzira zaumulungu wina aliyense wa m’zana lathu,” anatero katswiri wa zaumulungu Professor Georg Huntemann. Bonhoeffer, chiwalo chotsogolera cha “Tchalitchi cha Confessional,” anaikidwa m’ndende ndi a Nazi mu 1943 ndipo anaphedwa mu 1945 kaamba ka kupezedwa kukhala wophatikizidwa mu pangano la kupha Hitler. Huntemann wanena kuti Bonhoeffer angakhale anali kokha wokonzanso watsopano wa zosowa za tchalitchi. Onani kugwidwa mawu kotsatiraku kuchokera ku ena a mauthenga ake. Dzifunseni inu eni: Kodi nchiyani chimene kulabadira mawu ake kukatanthauza ku Tchalitchi cha Lutheran? ku tchalitchi changa?

“M’chipembedzo kokha chinthu chimodzi chiri chofunika kwambiri, chakuti chikhale chowona.” Ichi chimavomerezana ndi chimene Yesu ananena kuti: “Mulungu ndi Mzimu: ndipo omlambira iye ayenera kumlambira iye mu mzimu ndi m’chowonadi.”a—Yohane 4:24; onaninso Yohane 8:32; 14:6; 16:13.

Kodi muli otsimikizira kuti chirichonse chimene tchalitchi chanu chimaphunzitsa chiridi chowona? Kodi chimaphunzitsa kuti munthu ali ndi moyo wosafa—womwe sungakhoze kufa—kapena kodi chimavomerezana ndi Baibulo, lomwe limanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa”? (Ezekieli 18:4, 20) Kodi tchalitchi chanu chimakuphunzitsani kuti Mulungu alibe dzina kapena kuti amatchedwa Yesu, kapena kodi chimavomerezana ndi Baibulo, lomwe limanena kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu YEHOVA, ndinu wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi”? (Masalmo 83:18) Kodi tchalitchi chanu chimakuphunzitsani inu kuti anthu abwino onse adzatengedwa kupita kumwamba pamene dziko lapansi lidzawonongedwa ndi moto, kapena kodi chimavomerezana ndi Baibulo, limene limanena kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha”?—Masalmo 37:29; onaninso Masalmo 104:5.

“Icho [tchalitchi] chiyenera kumenyera kaamba ka kuyera kwa chiphunzitso.” Ichi chimavomerezana ndi chimene Yesu ananena kuti: “Chenjerani ndi chotupitsa mkate . . . , chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.”—Mateyu 16:12, NW; onaninso 1 Akorinto 5:8.

Kodi tchalitchi chanu chimavomereza “kuyera kwa kulongosola kwa munthu aliyense payekha,” kapena kodi chimachita m’chigwirizano ndi langizo la umulungu limene limati: “Abale yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsana, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzitsa inu; ndipo potolokani pa iwo”?—Aroma 16:17; onaninso 2 Timoteo 2:16-18; 2 Yohane 9, 10.

“Pa tsiku la Chimweruzo, Mulungu sadzatifunsa ife kwenikweni kuti: Kodi mwachita madyerero a mapwando a Kukonzanso kokhumbirika, koma m’malomwake: Kodi mwamvetsera ku Mawu anga ndi kuwasunga iwo?” Ichi chimavomerezana ndi chimene Yesu ananena kuti: “Abale anga ndiwo amene akumva mawu a Mulungu, nawachita.”—Luka 8:21; onaninso Mateyu 7:21; Yohane 15:14.

Kodi tchalitchi chanu chimaika kugogomezera kokulira pa mwambo, ndi nyumba kuposa ndi mmene chimachitira pa kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu? Kodi chiŵerengero cha opezeka pa tchuthi cha pa kanthaŵi pa tchalitchi chimalingaliridwa kukhala chokwanira, mosiyana ndi uphungu wa “osaleka kusonkhana kwathu pamodzi . . . monga momwe muwona tsiku [lachiŵeruzo] liri kuyandikira”?—Ahebri 10:25.

Kodi tchalitchi chanu chimakusonkhezerani kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, chikumakupatsani inu chithandizo chaumwini m’kumvetsetsa ilo ndi kupereka chisonkhezero cha kuchita chimene chiri chofunika?

“Chipembedzo chiri ntchito, mwinamwake yomwe iri yovuta koposa ndipo ntchito yoyera kwenikweni imene munthu angaichite.” Ichi chimavomerezana ndi chimene Yesu ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.”—Yohane 4:34.

Kodi tchalitchi chanu chimakuuzani inu kuti ntchito ya Mulungu kaamba ka Akristu lerolino iri kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu . . . m’dziko lonse kaamba ka umboni kwa mitundu yonse”? (Mateyu 24:14; onaninso Mateyu 28:19.) Kodi chimakufulumizani inu kugawana uthenga wa Ufumu waulemerero umenewu ndi “yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu”?—1 Petro 3:15.

Kwenikweni m’zitsanzo zomwe ziri pamwambazo, Bonhoeffer anapatsa tchalitchi chake ziganizo zabwino. “Koma kodi nchifukwa ninji mawu ake, a kudandaulira kwa kukonzanso kwake ku tchalitchi, amangopita kotheratu popanda kulabadiridwa?” Anafunsa tero Huntemann. Lapadera kwakukulu, ngakhale kuli tero, liri funso lakuti: Nchifukwa ninji mawu okhala ndi ulamuliro a Kristu Yesu amapita popanda kulabadiridwa pa mlingo wokulira?

Katswiri wa maphunziro a zaumulungu Ulrich Betz wanena kuti chitaganya cha mu West German chimalingalira ndi kuchita m’njira ya “pambuyo pa Chikristu, osanena za njira ya Chikristu.” Tchalitchi cha chiLutheran chiyenera kulandira kupatsidwa mlandu kaamba ka chifupifupi ziwalo mamiliyoni 25 za chitaganya chimenecho omwe ali a Lutheran. Ngakhale mtengo womwe umabala zipatso zoipa umapatsidwa mlandu, chotero chirinso tero tchalitchi chomwe chimabweretsa Akristu abodza. Yesu analongosola kuti: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wa mphuchi upatsa zipatso zoipa.”—Mateyu 7:16-18.

Pangani kuzindikira kowona mtima kumeneku. Kodi ndi zipatso za mtundu wotani zimene tchalitchi chanu chikutulutsa? Kodi chikuwongolera umunthu wa ziwalo zake? Kodi chikuchirikiza mtendere ndi umodzi pa mabanja, mudzi, ndipo mlingo wa dziko lonse? Kodi chiri mzati wotsutsa kugwiritsira ntchito molakwa kwa anamgoneka, chisembwere, ndi upandu? Kodi inu, mosasinkhasinkha, munganene kuti dziko likakhala malo abwino a kukhalamo ngati aliyense anali wa tchalitchi chanu?

Onani pa tsamba lotsatira chifukwa chimene a Lutheran ena mu Germany, pambuyo pa kupanga kufufuza kowona mtima koteroko, anatembenukira kwinakwake kaamba ka chitsogozo chauzimu.

Ngati Tchalitchi Chanu Chilephera Kuchitapo Kanthu, Kodi Mudzatero Nanunso?

Ngati, pambuyo pa kupanga kufufuza kowona mtima, inu muli osakondweretsedwa ndi zimene mukuwona, chitani zoposa kudandaula chabe. Mtola nkhani wina, polongosola pa ndemanga ya Karl Barth yakuti tchalitchi chiri ziwalo zake, anatsiriza mowona mtima kuti: “Ziwalo za tchalitchi . . . ziri za thayo kaamba ka chimene tchalitchi chimanena ndi kuchita.” Chotero dzifunseni inu eni: Kodi ndiri wofunitsitsa kugawana thayo kaamba ka chirichonse chimene tchalitchi changa chimanena ndi kuchita? Kodi ndingakhaledi wonyada kwenikweni ndi kukhala ndi ziwalo zonse za icho monga abale auzimu?

Pamene mukulingalira mafunso amenewa, musanyalanyaze kupatulika kwa Chivumbulutso 18:4, 8. Kulongosola pa ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, chonyansa kwa Mulungu, ilo limati: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake . . . [pakuti] miliri yake [idzadza] m’tsiku limodzi, imfa ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapsyerera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu woweruza ndiye wolimba.”

Inu mungakhulupirire motsimikizirika kuti tchalitchi chanu sichiri mbali ya chipembedzo chonyenga chimene Mulungu wanena kuti adzachiwononga posachedwapa. Koma moyo wanu umadalira pa kukhala wodzitsimikizira 100 peresenti. Kodi muli tero?

Chipembedzo chonyenga chiribe mtsogolo, kapena ngakhale awo omwe amachichirikiza. Chipembedzo chowona chidzakhala kosatha, limodzi ndi awo omwe amachichita icho. Pangani chosankha chanu mwatsatanetsatane.

[Mawu a M’munsi]

a Kugwidwa Mawu konse kuli kochokera mu King James Version.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

Pa misonkhano yawo—mwachitsanzo, mogwiritsira ntchito zitsanzo monga momwe zikuwonedwera pano—Mboni za Yehova zimapatsidwa malangizo ogwira ntchito a kugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo mu moyo wa tsiku ndi tsiku. Kuitana kozindikirika kwa mawu a chowonadi kwa lipenga kumeneku, kosasokonezedwa ndi kusanganizana kwa ndale za dziko kapena kusiya kwa ziphunzitso, kumalimbikitsa chiyembekezo chawo kaamba ka mtsogolo ndi kuwasonkhezera ku ntchito za Chikristu ndi michitidwe. Pezekaniko ku misonkhano ndi kudziwonera nokha!

[Bokosi patsamba 30]

Omwe Anali a Lutheran Kale Akulongosola Chifukwa Chimene Iwo Ali Mboni za Yehova Tsopano

“Chomwe chinandikondweretsa ine poyamba ponena za Mboni za Yehova chinali udongo ndi kuwona mtima komwe ndinawona pa imodzi ya misonkhano yawo. Ndikulimbikitsa ena kupezeka ku umodzi kuti akadziwonere okha chikondi chenicheni pakati pa Mboni.”—W. R., yemwe kale anali wosunga ndalama za tchalitchi.

“Ndinasonkhana ku tchalitchi Sande iriyonse. Koma uthengawo, kwakukulukulu wa utali wa mphindi 20, sunakhoze kuyankha mafunso anga onena za chifuno cha moyo kapena ponena za moyo pambuyo pa imfa. Mboni za Yehova zinandipatsa ine yankho lolondola kuchokera m’Baibulo, ndipo ndinakhoza kulankhula ndi iwo pa maziko a kukambitsirana kwachindunji. Zambiri zifunikira kuphatikizidwa mu utumiki wa umulungu kuposa kokha kungovomereza ku mabelu a tchalitchi m’mawa mwa Sande iriyonse, kuimba nyimbo, ndi kumvetsera ku uthenga. Palibe wofufuza zotsimikizirika aliyense kaamba ka chowonadi amene angakhale wokhutiritsidwa ndi chimenecho! Iye amafuna kuchita chinachake.”—E. B., yemwe anali kale mphunzitsi wa Sukulu ya pa Sande.

“Ntchito yanga monga mkulu wa tchalitchi siinaphatikizepo nkomwe nkhani za m’Baibulo, koma kokha nkhani za malonda zenizeni. Chomwe chinandithandiza ine kwakukulukulu chinali kuphunzira dzina la Mulungu, Yehova, dzina limene sindinamvepo likutchulidwa ku tchalitchi. Ndinakondweretsedwa ndi unyinji wa chowonadi wopezeka m’Baibulo.”—E. M., yemwe anali kale mkulu wa tchalitchi.

“Nthaŵi yoyamba imene Mboni za Yehova zinalankhula kwa ine, kusiyana [pakati pa iwo ndi ife] kunawoneka. Chenicheni chakuti anafuna kulankhula ndi ine ponena za Baibulo chinali chatsopano kotheratu ndi chachilendo. Funso langa loyamba linali lakuti kaya iwo ankalipiridwa kaamba ka ntchito yawo. Iwo anati ayi. Funso langa lachiŵiri linali lakuti kaya iwo anamenyako mkati mwa nkhondo. Iwo analongosola kuti Mboni zambiri zinali mu ndende za chibalo. Potsirizira pake, ndinapeza anthu ofunitsitsa, ngati kuli kotheka, kufa kaamba ka chikhulupiriro chawo.”—H. M., yemwe kale anali wosunga ndalama za tchalitchi.

“Pamene ndinafunsa pasitala wanga kuti alongosole chifukwa chimene pasitala aliyense anali ndi kulongosola kwakekwake, iye anati: ‘Pasitala aliyense ali ndi kuyenera kwa kuwona Mulungu m’njira imene idzamulola iye kuikidwa ku kugwiritsiridwa ntchito kwabwino mu mpingo.’ Pambuyo pake ndinatenga mbali m’kupezeka ku misonkhano ya mipingo iŵiri yosiyanasiyana ya Mboni za Yehova. Chomwe chinandigwira ine chinali kugwirizana kotheratu pakati pawo. Ndipo zofalitsidwa zinali ndi nsonga zophulapo kanthu, zochirikizidwa nthaŵi zonse ndi malemba a m’Baibulo omwe ukakhoza kuŵerenga mwamsanga kuchokera m’Baibulo lako! Ndi kusiyana kotani nanga ku mauthenga ambiri omwe ndamvapo!”—U. P., yemwe kale anali wogwira ntchito ya mayanjano ndi namwino wa parish.

[Chithunzi patsamba 29]

Misonkhano ya chigawo imasonkhezera Mboni za Yehova kuchita ntchito ya kulalikira Ufumu wa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena