Lingaliro Labaibulo
Kuchotsa Mimba—Yankho ku Chiŵerengero cha Anthu Chopambanitsa?
KAYA ngati chingakhale lamulo la dziko kapena chosankha cha aliyense payekha, kuchotsa mimba kwakhala chochititsa chofala cha kulamulira chiŵerengero cha anthu ponse paŵiri nthaŵi zakale ndi zamakono.
Cholembedwa cha mu nyuzipepala ya ku Canada chokhala ndi mutu wakuti “Chowawa cha ku China chiri kuchotsa mimba 53 miliyoni” chikugwira mawu Chigawo cha Zaumoyo wa Unyinji mu China kukhala chikusimba kuti chimenechi chiri chiŵerengero chozizwitsa cha nyengo kuchokera mu 1979 kufika ku 1984. Unyinji wonse umenewu wa kuchotsa mimba kwa zaka zisanu umalingana ndi kuposa kuŵirikiza kaŵiri kwa chiŵerengero cha anthu a mu Canada!
Japan akuyerekeza kuti 30 peresenti ya okhala ndi pakati 2.1 miliyoni chaka chirichonse m’dziko limenelo amachotsa mimba. Ena a ana osabadwa amenewa amakumbukiridwa ndi miyala yaing’ono, maplasitiki, kapena zinthu zowumba zoikidwa m’makachisi a chiBuddha modutsa dziko lonselo.
Ku mbali ina ya dziko, mu Sweden, kuchotsa mimba mofunidwa kwaloledwa chiyambire 1946 kaamba ka “zamankhwala, mankhwala a zamayanjano, makhalidwe aumunthu ndi zifukwa za kubala kapena kaamba ka kuvulazika kwa mwana wosabadwa.” Tsopano, monganso m’maiko ena, akazi ambiri a chiSwedish amawona kuchotsa mimba monga njira yolandiridwa mwa mayanjano ndipo yofala ya kulekezera mlingo wa mabanja awo.
Kachitidwe Kakale Kofala
Mu Atene wakale, kuchotsa mimba kunkagwiritsiridwa ntchito kulamulira kakulidwe ka chiŵerengero cha anthu. “Kuika polekezera kwaufulu kwa banja kunali kachitidwe kanthaŵiyo, kaya mwakumwa mankhwala oletsa kutenga mimba, mwakuchotsa mimba, kapena mwakupha ana,” molingana ndi wodziŵa za mbiri yakale Will Durant mu The Story of Civilization.
Kuchotsa mimba kunalinso kofala mu Ufumu wa Roma. Kaamba ka chifukwa chotani? Durant akupitiriza kuti: “Akazi anakhumba kukhala okongola mwa kugonana kuposa mwa kukhala ndi mimba; mwachisawawa chikhumbo cha ufulu wa aliyense chinawoneka kukhala chikumachita mosiyanasiyana ndi zifuno za fuko. . . . Kwa awo omwe anakwatira, ochulukira anawoneka kukhala atachepetsa mabanja awo mwa kuchotsa mimba, kupha ana, kachitidwe ka kuchinjiriza kutuluka kwa ubwamuna, ndi mankhwala oletsa kutenga mimba.” Kodi kuwonjezeka m’kuchotsa mimba m’nthaŵi yathu sikuli kaamba ka zifukwa zofananazo?
Kawonedwe ka Akristu Oyambirira
Mosiyana kwenikweni, Akristu oyambirira anatenga kaimidwe kolimba motsutsana ndi kuchotsa mimba. Durant akuwonjezera kuti: “Kuchotsa mimba ndi kupha ana, komwe kunkachirikiza chitaganya chachikunja, kunali koletsedwa kwa Akristu monga kulingana ndi kupha munthu.” Chotero pamene kuli kwakuti kuika polekezera kwa banja kunakhala chikhoterero chapadera cha mayanjano a ponse paŵiri mbali ya Agriki ndi Aroma, gawo la Chikristu lidaima molimba pa lamulo losamalitsa la makhalidwe abwino lomwe linamanga ulemu kaamba ka kupatulika kwa moyo. Monga mmene zinaliri mu Israyeli wakale, ana anali chizindikiro cha madalitso a Mlengi. Wamasalmo analongosola kuti: “Tawonani! Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake.”—Masalmo 127:3.
Chiri chowonekera kuchokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo, kuti Yehova, “magwero a moyo,” amazindikira cholungama ku moyo wa mwana wosabadwa. Motani? Choyamba, Baibulo limasonyeza kuti iye amawona wosabadwayo kukhala woposa chabe kachidutswa ka chiwalo. Chikondwerero cha Mulungu mkakonzedwe kake kodabwitsa ka kulenga chalongosoledwa ndi wamasalmo mwanjirayi: “Pakuti [Yehova] munandiwona ine m’mimba ya amayi wanga . . . ndisanawumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’bukhu mwanu.”—Masalmo 36:9; 139:13-16.
Kuwonjezerapo, Mulungu amaŵerengera mlandu munthu yemwe mwangozi amasokoneza kachitidwe kachibadwa ka zinthu zophatikiza mwana wosabadwa. Dziŵani kuti Lamulo la Mose linaika thayo lokulira pa oterewa, likumanena kuti: “Akayambana amuna nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kupwetekwa; alipe ndithu monga momwe amutchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oŵeruza. Koma ngati kupweteka kukalipo, udzipereka moyo kulipa moyo.”—Eksodo 21:22, 23, American Standard Version.
Tsopano ngati Yehova amawona kusokoneza kwangozi koteroko kwa mwana wosabadwa kukhala nkhani yokhala ndi zotulukapo zoipa zoterozo, ndi mlandu wokulira chotani nanga umene ukakhalapo ndi kusokoneza kwadala, monga m’nkhani ya kuchotsa mimba! Kachiŵirinso, popeza kuti Mulungu sanapatse malekezero ponena za msinkhu wa mwana wosabadwa mu lamulo lake lolongosoledwa pa Eksodo 21, kutsutsana kozikidwa pa msinkhu kukakhala kokayikiritsa.
Yankho ku Chiŵerengero cha Anthu Chopambanitsa
Chikhalirechobe, ena angalingalire kuti ndi kuwonjezeka kwa kuperewera kwa chakudya, kusoweka kwa nyumba zabwino, ndi kuperewera kwa kupereka madzi abwino, kuchotsa mimba kwa apa ndi apo monga chochititsa kulamulira chiŵerengero cha anthu kukakhoza kuchotsako chididikizo pa mbadwo womwe ukudza. Komabe, kodi kumeneko kuli njira yokha ya kulinganiza chiŵerengero cha dziko cha anthu ndi malo ozungulira a dziko lapansi?
Zaka 6,000 zapitazo, Yehova Mulungu analongosola chifuno chake kulinga ku chiŵerengero cha dziko cha pulaneti ya Dziko Lapansi. Yehova analengeza kwa anthu okwatirana oyambirira aŵiri kuti: “Mubalane muchuluke, mudzaze dziko lapansi ndi kuligonjetsa.” (Genesis 1:28) Dziŵani kuti chifuno cholongosoka cha Mulungu chiri kudzaza, osati kudzaza mopambanitsa, dziko lapansi. Mlengi adzafikiritsa cholinganiza cha chiŵerengero cha dziko—kusungirira chiŵerengero cha dziko cholondola, kulinganiza kwa anthu ndi zowazungulira, ndi kutulutsa kwa zakudya zokwanira.—Yesaya 65:17-25.
Chiri cholondola kutsiriza kuti Mlengi wamphamvu zobalira za anthu iyemwini adzayendetsa molondola kugwiritsira ntchito kwake kuti afikiritse kulinganiza kwaungwiro kumeneko. Sikudzakhala chifuno cha kuchotsa mimba kuti aike malire ku kukula kwa chiŵerengero cha anthu. Yehova kupyolera mu Ufumu wa Mwana wake, Kristu Yesu, adzatsimikizira kuti dziko lapansi ladzazidwa bwino lomwe ndi anthu omvera okhala kuzungulira dziko la paradaiso.—Yesaya 55:8-11; Chivumbulutso 21:1-5.
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Kuchotsa mimba ndi kupha ana . . . kunali koletsedwa kwa Akristu monga kolingana ndi kupha munthu.”—Will Durant, katswiri wa mbiri yakale
[Chithunzi patsamba 24]
“Pa nthaŵi imene kamwana ka m’mimba kali ndi miyezi isanu ndi umodzi iko kangakhoze kuwona, kumva, kudziŵa, kulawa ndipo ngakhale kuphunzira.”—Dr. T. Verny, mkonzi wa bukhu lakuti “The Secret Life of the Unborn”