Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 7/8 tsamba 11-13
  • Ndinaphunzira Kulamulira Mkwiyo Wanga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinaphunzira Kulamulira Mkwiyo Wanga
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ukwati ndi Nsanje
  • Kusintha
  • Chitsutso cha Banja
  • Kulamulira Mkwiyo Wanga
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizipewa Kupsa Mtima?
    Galamukani!—2009
  • Ndinasiya Khalidwe Lokakala Mtima
    Galamukani!—2003
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 7/8 tsamba 11-13

Ndinaphunzira Kulamulira Mkwiyo Wanga

CHOCHITIKA chinali chozolowereka: nyumba ya maseŵera ya ku Europe yofanana ndi zina zochulukira zomwe ndinaseŵera monga katswiri wodziŵa zoimba. Monga mwa nthaŵi zonse, mabwenzi anga ndi ine tinamwerekera m’zakumwa zoledzeretsa. Sindikhoza ngakhale kukumbukira chifukwa chimene ena a odzawonerera anatiwukira.

Ndimakumbukira kuulika kwa nkhonya. Ndinali wachichepere ndi wamphamvu ndipo ndinamenya mmodzi wa odzapenyerera mwamphamvu kwenikweni kotero kuti iye anagwera pa tebulo. Kenaka ndinanyamula mpando ndi kuyamba kumenya enawo. Mphindi zoŵerengeka pambuyo pake, chipindacho chinali chopanda anthu—kusiyapo kokha thupi losakhoza kuchita kanthu liri gone pansi. Nditawopsyedwa ndi kusowa chochita, ndinathaŵira kunyumba kukatsanzika mkazi wanga, popeza ndinakhutiritsidwa kuti ndidzamangidwa ndi kupatsidwa mlandu wakupha munthu!

Iyi, mwatsoka, siinali nthaŵi yoyamba pamene mkwiyo wanga unatulutsidwa chotero. Koma kuti muyamikire nchifukwa ninji chimenechi chinali tero, inu muyenera kumvetsetsa mwapang’ongo ponena za chiyambi changa. Ndinaleledwa m’banja la a Gypsy—osati la mtundu wokonda kuyendayenda, popeza banja langa nthaŵi zonse linakhala m’nyumba yawo. Atate anali oledzera kaŵirikaŵiri ndipo a nsanje yaikulu kwa amayi anga. Phokoso la chiwawa linali lofala m’nyumba yathu.

Njira ya moyo yomwe ndinatsatira pambuyo pake inandiwunikiranso ine ku zizolowezi zoipa zambiri. Atate ankapeza ndalama yodyera monga woimba nyimbo, ndipo ndinawatsatira iwo mwamsanga pamene ndinafika pa msinkhu wa zaka zisanu ndi zitatu. Ndinaphunzira kuseŵera accordion, ndipo pamene ndinali wa zaka 13, ndinakhoza kuwonekera monga woimba yekha kapena ndi oimba ena. Ichi chinatanthauza kuseŵera mu mahotelo, nyumba za moŵa zapoyera, ndi pa madyerero a maukwati, kaŵirikaŵiri usiku wonse. Mwamsanga ndinaphunzira kumwa zakumwa zoledzeretsa ndi kusuta.

Ukwati ndi Nsanje

Palibe nchimodzi chomwe cha izi chinandithandiza kukulitsa umunthu wa bata. Ngakhale ukwati sunandikhazikitse pansi ine. Pa msinkhu wa 19 ndinakwatira mtsikana wokongola wa chiGypsy. Tinachita molingana ndi mwambo wa chiGypsy, tikumakhala ndi phwandolo likuchitidwa ndi mfumu ya banja, m’malo mwa mtsogoleri wa chipembedzo. Ndimakhoza kukumbukira iye akumatenga dzanja langa ndi dzanja la mkwatibwi wanga ndi kuwagwirizanitsa iwo pamodzi zikhatho zathu ziri m’mwamba. Iye kenaka anathira zakumwa zoledzeretsa m’chikhatho chirichonse. Ndinayenera kumwa kuchokera ku chikhatho cha mkwatibwi wanga ndipo iye kuchokera ku changa. Kuchokera pamenepo kupitirizabe tinalingaliridwa ndi chitaganya cha anthu a chiGypsy monga okwatirana mwalamulo, ngakhale kuti pambuyo pake tinakwatirana m’bwalo la zamaseŵera la m’mzinda kuti ukwati wathu ulembetsedwe.

Mwamsanga pambuyo pake ndinadzipeza inemwini ndikumadzimva wa nsanje ya chiwawa yofanana ndi imene atate wanga anawonetsa. Ndinayamba kumenya mkazi wanga wachichepere, nthaŵi zina kufika ku mlingo wa kaŵiri pa mlungu! Mosakaikira ichi chinathandizira ku kumwa kwanga mokulira kuposa nkalelonse. Ichi, monga chotulukapo, chinangokulitsa mkwiyo wanga. Panthaŵi imodzi ndinkamwera m’nyumba ya atate wanga limodzi ndi mabwenzi anga oŵerengeka achiGypsy. Mbale wanga wachikulire anayamba kuneneza mkazi wanga. Ndiri chiledzerere monga mmene ndinaliri, ndinathamangira kunyumba, kugwira mkazi wanga pa dzanja ndi kumkoka kuchoka pa kama m’zovala zake za usiku kupita mtunda wonsewo kunyumba ya atate wanga. Ndinampangitsa iye kulumbira pamaso pa mtanda kuti chimene mbale wanga wachikulireyo ananena sichinali chowona!

Komabe, ngakhale kuti analumbira ku chirichonse, ndinakhala wokwiya mowonjezereka. Ndinathamangira kunyumba, kutenga nkhwangwa, ndi kuyamba kuphwanya mazenera a nyumba. Mbale wanga wina anadza kuyesa kundiletsa. Ndinamkankha iye mwachiwawa kotero kuti anagwa pansi ndi kuthyola dzanja lake.

Kusintha

Mkwiyo wanga wachiwawa unapita wosasamaliridwa kwa nthaŵi yotalikira kufikira chochitika chotchulidwa poyambirirapo, pamene ndinalingalira kuti ndinapha munthu. Pambuyo pa kutsanzika mkazi wanga, ndinapita ku tchalitchi cha Roma Katolika cha kumaloko, kumene ndinagwada pansi kutsogolo kwa khomo lalikulu lolowera ndipo, m’misozi ndinapemphera kwa Mulungu kaamba ka chikhululukiro chake. Ndinalonjeza kuti sindidzabwerezanso kuchita chinthu choterocho! Ku chimasuko changa chachikulu, ngakhale ndi tero, ndinaphunzira kuti munthuyo sanafe koma anangovulazika.

Mwa njira ina, ndinadzimvabe wopsyinjika kwambiri ndi wopanda chochita. Masiku atatu pambuyo pake ndipo ndidakali wovutikabe, ndinkayenda pa sitima kupita ku ntchito. Mwamuna wachichepere anayamba kulankhula kwa ine ponena za Ufumu wa Mulungu, boma limene lidzathetsa mavuto onse omwe amakantha mtundu wa anthu—boma limene lidzachotsapo pa dziko lapansi matenda, imfa, ndi chisoni! Mwamuna wachichepereyo anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Popeza kuti ndinakhulupirira mwa Mulungu, ndinamvetsera mwaulemu. Koma chimene mwamuna wachichepereyo ankandiwuza chinawoneka kukhala chosakhala chenicheni. “Kodi ndani yemwe akakhoza kuchita zonsezi?” Ndinamfunsa tero. Iye anayankha kuti, “Mulungu Wamphamvuyonse adzatero.”

Yankho limeneli linandikhutiritsa ine kotheratu. Iye anandipatsanso kabukhu ndi kulonjeza kuchezera nyumba yanga. Asanatero, Mboni zina ziŵiri zinandichezera ndi kundibweretsera mabukhu akale atatu, Creation, Reconciliation, ndi Riches, onse ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Pamene mwamuna wachichepere yemwe ndinakumana naye mu sitima potsirizira pake anandichezera, tinayamba kuphunzira bukhu la “Mulungu Akhale Wowona.”a

Ndinapanga kupita patsogolo kofulumira. Mkati mwa milungu isanu ndi umodzi yokha ndinazindikira kuchokera m’kuŵerenga kwanga kwa zofalitsidwazi kuti tchalitchi changa chinalibe chirichonse chondipatsa ine. Ndinapita kolembetsera maina ndi kufunsa kuti dzina langa lichotsedwepo pa ndandanda ya ziwalo zawo.

Chitsutso cha Banja

Zinayamba kuvuta pa ine, ngakhale ndi tero, kotero kuti ndinafunikira kupanga masinthidwe ena mu umunthu wanga. Ndinadziŵa mkazi wachikulire pa malo anga a ntchito yemwe anali Mboni. “Kodi Mboni zimatengamo mbali m’zamaseŵera ndi mapwando aukwati?” Ndinamfunsa tero. “Inde, zimatero,” iye anayankha tero. “Koma iwo amachita m’njira Yachikristu.” Ndinamfunsa iye chimene chimenecho chinatanthauza.

“Iwo samaledzera; ngakhale kufuula kapena kusuta.”

Kuchokera pa nthaŵiyi kupitirizabe, sindinagwire ndudu kachiŵiri. Ndipo m’mwezi wachitatu wa kuphunzira kwanga Baibulo, ndinaleka mwadzidzidzi kuseŵera ndi mabwenzi anga oipawo. Ndinazindikira kuti kuyanjana koipa koteroko kukaletsa kupita kwanga patsogolo.

Chimenecho chinatanthauza kupeza njira yatsopano ya kukhalira. Chotero ndinagwira ntchito monga woyala njerwa. Ntchito yanga yatsopano, ngakhale ndi tero, siinandibweretsere ndalama zomwe kugwira ntchito monga woimba kunadzetsa. Chotero mkazi wanga, atate wanga, abale anga—chifupifupi onse omwe anandidziŵa ine—anali otsutsana ndi ine ndipo anayesera kundikakamiza ine kubwerera ku njira yanga yakale yamoyo. Ndi thandizo la Yehova, ndinaleka kumwa mopambanitsa zakumwa zoledzeretsa ndipo ndinayamba kuyesera kulamulira mkwiyo wanga.

Mungalingalire kuti mkazi wanga akanakhala wosangalatsidwa ndi masinthidwe anga, koma sizinali tero. Popeza kuti sindinamumenyenso iye kapena kutsutsana naye nkomwe, iye anadzimva kuti sindinamkondenso! Kumeneko ndiko kulingalira kwa mkazi wa chiGypsy. Kenaka Krisimasi inayandikira ndipo sindinapange makonzedwe alionse a kusangalalira iyo. Ndinaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti uku sikuli kukondwerera komwe Mulungu amakuvomereza.b Mkazi wanga, ngakhale kuli tero, sanamvetsetse chirichonse cha ichi. Iye anakwiya kwambiri kotero kuti anandisiya ine, akumatenga limodzi naye ana athu anayi. Anakhala ndi makolo ake, amene kenaka ananditumizira ine uthenga wotsatirawu: Leka chipembedzo chako chatsopano kapena ngati sitero sudzalowanso m’nyumba mwathu kachiŵirinso ndipo mkazi wako sadzabwerera kwa iwe!

Uku kunali kudidikiza kwamphamvu chifukwa chakuti ndinamkonda mkazi wanga ndi ana kwambiri. Ndinakana kuleka, ndipo milungu iŵiri pambuyo pake mkazi wanga ndi ana anabwerera kunyumba—popanda kuyesera kwa kuwaitana kulikonse. Mwamsanga pambuyo pake, kokha miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pa kukumana ndi mwamuna wachichepere ameneyo, ndinabatizidwa monga mboni ya Yehova.

Kulamulira Mkwiyo Wanga

Ngakhale kuti tsopano ndinali Mkristu wobatizidwa, kulamulira mkwiyo wanga sikunali kopepuka. Komabe, ndi kuphunzira kwa Baibulo ndi pemphero losamalitsa, Yehova anandipatsa ine mphamvu yofunika.

Ndinakhozanso kupirira chitsutso cha mkazi wanga. Kaŵirikaŵiri iye ankandiseka pamene ndinayesera kuphunzira Baibulo. Pamene ndinayesera kugawana naye chinachake chomwe ndinkaŵerenga, iye ankayamba kuimba m’liwu lokwezeka kuti andisokoneze! M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale kuli tero, umunthu wanga wosinthidwa unali ndi chiyambukiro pa iye. Zaka ziŵiri pambuyo pake, iye nayenso anakhala mlambiri wokhulupirika wa Yehova.

Papita nthaŵi yaitali chiyambire pamene ndinali pafupi kupha munthu m’nyumba ya maseŵera ija. Kuyambira pamenepo ndakhala ndi mathayo a kutumikira monga mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova ndi kupenyerera ana anga onse, kusiyapo mmodzi, akulandira chowonadi. Ndimagwira ntchito ndi mpingo wa Akristu enieni omwe samandiwopa ine koma omwe amagwira ntchito mofunitsitsa ndi ine mu ntchito yathu yolalikira.

Inde, ndiri wosangalatsidwa kwambiri kuti chowonadi cha Baibulo chinandithandiza ine kugonjetsa mkwiyo wanga wachiwawa.—Popeza kuti wolemba wa nkhaniyi amakhala m’dziko kumene Chikristu chiri choletsedwa ndi boma, iye wasankha kukhala wosadziŵika ndi dzina.

[Mawu a M’munsi]

a Lerolino zofalitsidwa zonsezi zinaleka kusindikizidwa.

b Onani chofalitsidwa cha Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, mutu 25.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Pa msinkhu wa 19 Ndinakwatira mtsikana wa chiGypsy

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Ndinayamba kumenya mkazi wanga wachichepere, nthaŵi zina kaŵiri pa mlungu

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Iwo samaledzera; ngakhale kufuula kapena kusuta”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena