Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 7/8 tsamba 9-11
  • Ubongo—“Woposa Kompyuta”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ubongo—“Woposa Kompyuta”
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubongo Wodabwitsa Koposa Wonse
  • Unapangidwa ndi Ndani?
  • Katswiri Woona za Ubongo Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
    Galamukani!—2017
  • Kodi Mumadziwa Kuti Tili ndi Mitsempha Ina Imene Imagwira Ntchito Ngati Ubongo?
    Galamukani!—2017
  • Bongo Wodabwitsa Umenewo wa Khanda!
    Galamukani!—1987
  • Linapangidwa Kuti Likhale Kosatha
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 7/8 tsamba 9-11

Ubongo—“Woposa Kompyuta”

CHIWALO china chabwino koposa chiri ubongo wamunthu. Iwo, limodzi ndi dongosolo lotumiza ndi kulandira mawu lonse lathunthu, kaŵirikaŵiri umayerekezedwa ku kompyuta yopangidwa ndi munthu. Ndithudi, makompyuta anapangidwa ndi anthu ndipo amagwira ntchito mogwirizana ndi kutsatira kumodzi ndi kumodzi kwa malangizo oikidwiratu ndi kulinganizidwa kwa munthu. Komabe, anthu ambiri amakhulupirira kuti palibe nzeru yomwe inali ndi thayo la “kulumikiza” ndi “kulinganiziratu” kwa ubongo wa munthu.

Ngakhale kuti ali ofulumira mokulira, makompyuta amachita kokha ndi unyinji umodzi wa chidziŵitso pa nthaŵi imodzi, pamene kuli kwakuti dongosolo la kulandira ndi kutumiza la munthu limachita ndi mamiliyoni ochulukira a unyinji wa chidziŵitso panthaŵi imodzi. Mwachitsanzo, mkati mwa kucheza mu nthaŵi ya ngululu, inu mungasangalale ndi kawonekedwe ka malo kokongola, kumvetsera ku nyimbo za mbalame, ndi kununkhiza maluŵa. Kuzindikira kokondweretsa konseku kumatumizidwa pa nthaŵi imodzi ku ubongo wanu. Nthaŵi imodzimodziyo, unyinji wa chidziŵitso umabwera kuchokera ku zolandirira zizindikiro m’mapazi anu, kudziŵitsa ubongo ponena za kakhazikitsidwe ka nthaŵi ndi nthaŵi ka mwendo uliwonse ndi mkhalidwe wa mnofu uliwonse. Zokhumudwitsa zomwe ziri kutsogolo m’njira yopitamo zimadziŵidwa ndi maso anu. Pa maziko a chidziŵitso chonsechi, ubongo wanu umatsimikizira kuti sitepi lirilonse limatengedwa molongosoka.

Pa nthaŵiyo, chigawo chapansi cha ubongo wanu chimalamulira kugunda kwa mtima wanu, kupuma, ndi kugwira ntchito kwina kofunika. Koma ubongo wanu umachita ndi zambiri. Pamene muyenda, mungakhoze kuimba, kulankhula, kulinganiza zochitika zatsopano lino ndi zochitika zakale, kapena kupanga makonzedwe kaamba ka mtsogolo.

“Ubongo,” latsiriza tero The Body Book, “uli woposa kompyuta. Palibe kompyuta yomwe ingagamulepo kuti yasungulumwa kapena ikuwononga maluso ake ndipo ifunikira kuyamba pa njira yatsopano ya moyo. Kompyuta singasinthe mwadzidzidzi programu yake; isanapite m’njira yatsopano, munthu yemwe ali ndi ubongo afunikira kuilinganiza iyo. . . . Kompyuta singapume, kapena kulota masana, kapena kuseka. Iyo siingawuziridwe kapena kulenga. Iyo siingakhale ndi kuzindikira kapena kudziŵa tanthauzo. Iyo siingakhale ndi chikondi.”

Ubongo Wodabwitsa Koposa Wonse

Nyama zonga ngati njovu ndi zolengedwa zina zazikulu za m’nyanja ziri ndi ubongo waukulu kuposa uja wa munthu, koma m’kulinganiza ku mlingo wa thupi, ubongo wa munthu uli waukulu koposa onse. “Nyani,” walongosola tero Richard Thompson mu bukhu lake The Brain, “ali mwakuthupi wamkulu kuposa munthu komabe ali ndi ubongo wa kokha ukulu wa mbali imodzi mwa zinayi za wa munthu.”

Chiŵerengero cha njira zosiyanasiyana pakati pa minyewa ya ubongo (maselo a mitsempha) mu ubongo wa munthu chiri chokulira koposa. Ichi chiri chifukwa chakuti minyewa ya ubongo iri ndi cholowanecholowane wochulukira wa kulumikizanitsidwa; m’nyewa wa ubongo umodzi ungalumikizane ndi yoposa zikwi zana limodzi. “Chiŵerengero cha kulumikizanitsidwa kothekera mkati mwa ubongo wamakono chiri chabe ngati chosatha,” walongosola tero Anthony Smith mu bukhu lake The Mind. Icho chiri chachikulu “kuposa chiwonkhetso chapamodzi cha mbali za atom zomwe zimapanga chilengedwe chodziŵidwa,” akutero katswiri wa minyewa ya ubongo Thompson.

Koma pali chinachake chomwe chiri chozizwitsa koposa. Chiri njira imene cholowanecholowane wokulira ameneyu wa minyewa ya ubongo walumikizidwira yomwe imatheketsa anthu kuganiza, kulankhula, kumvetsera, kuŵerenga, ndi kulemba. Ndipo zinthu zimenezi zingachitidwe m’zinenero ziŵiri kapena zowonjezereka. “Chinenero chiri kusiyana kokulira pakati pa anthu ndi zinyama,” walongosola tero Karl Sabbagh m’bukhu lake The Living Body. Kulankhuzana kwa zinyama kuli kosavuta mwa kuyerekeza. Kusiyana, wavomereza tero wa nthanthi ya chisinthiko Sabbagh, “sikuli kokha kuwongokera kochepera m’kuthekera kwa nyama zina kupanga phokoso—iko kuli mkhalidwe wofunika womwe umapangitsa anthu kukhala anthu, ndipo umawonekera m’kusiyana kokulira m’kapangidwe ka ubongo.”

Kapangidwe kozizwitsa ka ubongo wa munthu kasonkhezera ambiri kupanga kugwiritsira ntchito kwabwino kwa mphamvu zake mwa kukhala akatswiri pa zopangapanga zina, kuphunzira kuseŵera ndi ziwiya zoseŵerera nyimbo, kuzolowera chinenero china, kapena kukulitsa luso lirilonse kumawonjezera chimwemwe ku moyo. “Pamene muphunzira luso latsopano,” akulemba tero Drs. R. ndi B. Bruun m’bukhu lawo The Human Body, “inu mukuphunzitsa minyewa yanu ya ubongo kulumikiza m’njira yatsopano. . . . kuchulukira komwe mudzagwiritsira ntchito ubongo wanu, kudzakhalanso kulongosoka kokulira komwe iwo udzakhala.”

Unapangidwa ndi Ndani?

Kodi chinachake cholinganizidwa mopambana chotero ndi molongosoka chonga dzanja, diso, ndi ubongo chingabwere mwangozi? Ngati munthu akulemekezedwa ndi kuyambitsa ziwiya, makompyuta, ndi mafilimu ojambula, motsimikizirika winawake afunikira kulemekezedwa kaamba ka kupanga dzanja lokhoza kusinthasintha, diso, ndi ubongo. “Yehova,” wamasalmo wa m’Baibulo ananena tero, “ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsya ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”—Masalmo 139:1, 14.

Kugwira ntchito kozizwitsa kwambiri kwa thupi la munthu kumachitika popanda kulingalira kwathu. Makope amtsogolo a magazini ino adzalongosola ena a mapangidwe ogwira ntchito ozizwitsa amenewa, ndiponso kaya ukalamba, kudwala, ndi imfa zingagonjetsedwe, kotero kuti tisangalale ndi moyo kosatha!

[Chithunzi patsamba 9]

Ubongo wa munthu umachita ndi unyinji wa chidziŵitso pa nthaŵi imodzi. Pamene muyenda, zolandirira zizindikiro miyendo ndi mikono yanu zimadziŵitsa ubongo ponena za kaikidwe ka nthaŵi ndi nthaŵi ka mkono uliwonse ndi mkhalidwe wa mnofu uliwonse

[Chithunzi patsamba 11]

Ubongo uli wocholowanacholowana mokulira ndi wokhoza kusinthasintha kuposa kompyuta

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena