Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 7/8 tsamba 20-22
  • Misonkhano Yachikristu—Nchifukwa Ninji Kupita ku Iyo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yachikristu—Nchifukwa Ninji Kupita ku Iyo?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nyumba za Ufumu—Zosiyana Motsitsimula
  • Misonkhano—Chiwiya Kukukhala wa “Umoyo M’chikhulupiriro”
  • Misonkhano—Yosangalatsa ndi Yokoka
  • Malo a Kuphunzira
  • Misonkhano Imapindulitsa Achinyamata
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Mmene Yehova Akutitsogolera
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 7/8 tsamba 20-22

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Misonkhano Yachikristu—Nchifukwa Ninji Kupita ku Iyo?

“Makolo anga anandipangitsa ine kupita ku tchalitchi,” anatero Christiaan, m’nyamata wachichepere m’dziko la Suriname. “Ine nthaŵi zonse ndinakhumba chinthu chokhoza kundinyowetsa pa Sande mmawa, kotero kuti ndikhale panyumba. Koma,” iye akuwonjezera ndi kumwetulira, “chinawoneka kuti mvula inkagwa kokha kuchokera pa Lolemba mpaka Loŵeruka.”

“M’nthaŵi yochepa chikhumbo changa cha kupita ku misonkhano ya tchalitchi chinatha. Pamene ndinawona mwaŵi wa kuleka, ndinawugwira iwo.”

CHRISTIAAN ali kutalitali ndi kupatulidwa. Atsogoleri achipembedzo kuzungulira dziko amachitira chisoni kusoweka kwa chikondwerero kumene achichepere ali nako m’misonkhano ya chipembedzo. Watero Simote Vea, kalaliki kuchokera ku chisumbu cha Pacific cha Tonga: “Chiŵerengero cha anthu achichepere opezeka ku tchalitchi . . . chikutsika.”

Nchifukwa ninji, ngakhale kuli tero, matchalitchi akulu akulepherera kukoka anthu achichepere? Lorine Tevi, chiwalo cha World Council of Churches, wavomereza kuti: “Kusoweka kokulira kuli maphunziro . . . Matchalitchi afunikira kuphunzira kuti maphunziro a zaumulungu afunikira kulankhula kwa onse.”

“Chimenecho chiri cholondola,” wavomereza tero Christiaan. “Anthu achichepere ochulukira amakhumba maphunziro omveketsedwa a chindunji a Baibulo. Komabe, m’malo mwa kukwaniritsa chosowa chimenecho, matchalitchi amamamatira ku miyambo yakale.” Annie wa zaka 13, wawonjezera kuti: “Tchalitchi chiri kuyimba kochuluka koma kuphunzira kochepera.” Barbara wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu zakubadwa mofananamo anachitira chisoni kusoweka kwa maphunziro mu tchalitchi. “Tsiku lina,” iye akukumbukira, “pasitala anandipatsa zithunzithunzi zolembedwa za Yesu. Anandiwuza ine kuzipaka utoto izo. Umenewo ndiwo unali utumiki!”

Nchosadabwitsa, kenaka, kuti achichepere ochulukira akuipidwa ndi mautumiki a tchalitchi. Kodi chimenechi chimatanthauza, ngakhale ndi tero, kuti misonkhano ya zipembedzo zonse iri kutaya nthaŵi? Mosiyanako, achichepere omwe agwidwa mawu pano anayamba kupezeka ku misonkhano ya chipembedzo kachiŵirinso! Chifukwa chake? Iwo anapeza chimene magazini ya U.S. Catholic inasimba zaka zingapo zapitazo: “Nyumba ya Ufumu iriyonse imapereka . . . maphunziro ochulukira pa mwezi koposa mmene zimachitira nyumba za Chikatolika chaka chonse.”

Nyumba za Ufumu—Zosiyana Motsitsimula

Nyumba za Ufumu? Inde, awa ali malo okumanirako a Mboni za Yehova, ofalitsa a magazini iyi. Kufufuza komwe kunachitika m’dziko la Suriname kunasonyeza kuti chifupifupi mmodzi mwa anthu atatu alionse opezeka ku misonkhano kumeneko ali a pakati pa zaka 12 ndi 20! Chofananacho chiri chowona m’maiko ena ochulukira—chiŵerengero chochulukira cha achichepere chikupezeka pa misonkhano pa Nyumba za Ufumu.

Christiaan akulongosola chifukwa chimene misonkhano kumeneko inamukokera iye: “Ndinasangalatsidwa kuwona mmene kaŵirikaŵiri Baibulo linkagwiritsidwira ntchito. Chirichonse chimene chinanenedwa chinali cholembedwa bwino kuchokera ku ilo. Misonkhano inali monga sukulu!” Ndithudi, Nyumba za Ufumu ziri ndi kosi ya misonkhano isanu ya mlungu ndi mlungu yomwe imaphunzitsa Akristu m’kuŵerenga, kuphunzitsa, ndi kugwiritsira ntchito Baibulo. Inu mudzapeza kuti misonkhano kumeneko iri motsitsimula yosiyana ndi mautumiki a ku tchalitchi.

Chikhalirechobe, achichepere ambiri angasinthidwe kuchoka pa lingaliro la mtundu uliwonse wa sukulu. Ngakhale achichepere ena omwe aleredwa ndi makolo Achikristu angataye chiyamikiro chawo kaamba ka misonkhano Yachikristu, akumadandaula kuti iri ‘yosungulumwa,’ ‘yotalika,’ kapena kuti kuchita chinachake—monga ngati kupenyerera wailesi ya kanema—kukakhala kosangalatsa kwambiri. Nchifukwa ninji, kenaka, chimene munthu wachichepere afunikira kuchotsako nthaŵi ku zosangalatsa ndi ntchito ya ku sukulu kuti akapezeke ku misonkhano Yachikristu?

Misonkhano—Chiwiya Kukukhala wa “Umoyo M’chikhulupiriro”

Mtumwi Paulo nthaŵi imodzi analongosola kuti “popanda chikhulupiriro chiri chosatheka kumukondweretsa [Mulungu].” (Ahebri 11:6) Iye chotero analimbikitsa Akristu kukhala “aumoyo m’chikhulupiriro.” (Tito 2:2) Kodi uphungu umenewu uli woyenerera kaamba ka anthu achichepere lerolino? Ndithudi uli! Mtsikana mmodzi wa zaka zakubadwa 15 anachiika mwa njira iyi: “Nthaŵi zina ndimalingalira kuti anthu achichepere ali ndi nthaŵi yovuta m’moyo. Tiri pakati pa anthu omwe amachita dama, anamgoneka, ndi kumwa.” Kodi ungamenyere zizoloŵezi zokulira zimenezi mwa ‘kudzipatula iwe mwini’ kwa Akristu anzako? (Miyambo 18:1) Kutalitali.

Misonkhano Yachikristu chotero imakwaniritsa kusowa kofunika. Imakuthandizani inu kukhala “athanzi m’chikhulupiriro”! Anatero Tertullian, wokhulupirira wa m’zana lachiŵiri: “Timasonkhana kuti tiŵerenge zolembedwa zathu zoyera . . . ndi mawu oyera timadyetsa chikhulupiriro chathu.” Mofananamo lerolino, misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu ingakhoze ‘kudyetsa chikhulupiriro chathu’ ndi kukulimbitsani. Nchosadabwitsa, chotero, kuti Akristu akulamulidwa: “Lolani tikhale olimba ndi osagwedezeka m’kulongosola chiyembekezo chathu, . . . osalephera pa misonkhano yathu, monga mmene ena amachitira.”—Ahebri 10:23-25, The New English Bible.

Misonkhano—Yosangalatsa ndi Yokoka

Ngakhale kuli tero, mu mbadwo uwu wa nzeru zopangapanga, achichepere ochulukira samafuna kokha kuphunzitsidwa koma kusangalatsidwa. Ndipo movomerezeka, misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu siiri kapangidwe kokometsedwa ka pa pulatifomu yoseŵerera kongopeka. Ichi sichikutanthauza, ngakhale ndi tero, kuti programuyo iri yosakoma ndi yosakondweretsa. Talingalirani: Kodi nchiyani chomwe chimapangitsa chakudya kukhala chosangalatsa? Kodi sichiri chakudya chodzetsa mphamvu ndi chosiyanasiyana, mabwenzi okondweretsa mozungulira tebulo, ndi bata la malo otizungulira? Chabwino, misonkhano Yachikristu motsimikizirika imakwaniritsa miyezo iyi kaamba ka chisangalalo.

Yodzetsa Mphamvu ndi Yosiyanasiyana: Misonkhano isanu imatumikira kupereka chakudya chauzimu chokhala ndi zofunikira zonse za thupi—kuchokera pa uphungu wonena za moyo wa banja kufika ku phunziro la maulosi. Kusiyanasiyana? Chabwino, nkhani ndi kukambitsirana kwa gulu kaŵirikaŵiri zimasinthanitsidwa ndi kufunsana ndi zitsanzo za umoyo. Janet wa zaka zakubadwa khumi ndi zisanu amakumbukira msonkhano wake woyamba: “Tiri pakatimpakati pa msonkhano ndinawuza amayi anga, ‘tiyeni tipite kunyumba.’ Ndinali wotopa ndi kukhala pansi. Koma kenaka achikulire ndi achichepere anayamba kusinthanasinthana kulankhula pa pulatifomupo. Ndinachikonda icho ndipo ndinakhala kufikira kumapeto.”

Mabwenzi Osangalatsa: Pambuyo pa kupezeka ku msonkhano wake woyamba, mtsikana wachichepere wotchedwa Carolina, wa ku Nicaragua, ananena kuti: ‘Ziwalo zachichepere zinandisangalatsa ine. Iwo anali aubwenzi ndi aulemu.’ Inde, pa Nyumba ya Ufumu mungapeze ubwenzi ‘wabwino ndi wosangalatsa.’ (Masalmo 133:1) Anita wa zaka zakubadwa khumi ndi zisanu ndi chimodzi chotero ananena kuti: “M’nyumba ya Ufumu, ndinapeza mabwenzi enieni.”

Malo Otizungulira Abata: “Nthaŵi zina ndimadera nkhaŵa ponena za vuto lina tsiku lonse,” akutero Simeon, wa zaka 14. “Koma m’Nyumba ya Ufumu, ndimaiwalako ponena za icho. Ndimadzimva wa mtendere mkati.” Misonkhano Yachikristu imawunikira mzimu wa Mulungu wachimwemwe ndi mtendere. (Afilipi 4:4-7) Ndipo mosiyana ndi kamangidwe kokometseredwa kochititsa chidwi ndi mkhalidwe wokopa wa pamalopo wokonzedwa mwamachenjera wa matchalitchi ambiri, Nyumba za Ufumu ziri zopepuka m’kamangidwe ndipo zimatheketsa malo ozungulira abata. Akutero Barbara wachichepere: “Mu Nyumba ya Ufumu, ndimadzimva kukhala womasuka ndi wolandirika.”

Malo a Kuphunzira

Chofunika koposa kuposa malo ozungulira, ngakhale kuli tero, chiri chimene mumaphunzira mwa kupezeka ku misonkhano pa Nyumba ya Ufumu. Kuchitira chitsanzo, lingalirani kokha umodzi wa misonkhano isanu, Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Inakhazikitsidwa mu 1943 kuphunzitsa Akristu mu luso la kulankhula poyera. Iyo iri sukulu ya dziko lonse, yokhazikitsidwa m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse, ndipo imapereka mwaŵi wolingana wa maphunziro. Ophunzira amalandira kuphunzitsidwa kofanana kaya ali anyamata kapena atsikana, akuda kapena oyera, olemera kapena osauka—kwaulere!

Bukhu lalikulu lophunziridwa liri Baibulo. Aphungu ofikapo amaphunzitsa ophunzira mmene angasonkhanitsire ndi kukulitsa chidziŵitso cha Baibulo ndipo kenaka kuchipereka icho mu mkhalidwe wokambitsirana. Bukhu lotchedwa Bukhu Lolangiza la Sukulu ya Utumiki wa Teokratikia limagwiritsiridwanso ntchito m’chigwirizano ndi sukuluyo. Maphunziro ake 38 amachita ndi nkhani zonga ngati “Kupanga Autilaini,” “Kugogomezera Ganizo ndi Kusintha Mawu,” ndipo amaphunzitsa kusankha mawu, katchulidwe ka mawu, ndi kalembedwe. Pamene wachichepere wotchedwa Terri anapereka bukhu limeneli kwa mlangizi wake wa Kalasi ya Kulankhula, iye anawuza ophunzira ena kuti: “Pambuyo pa milungu isanu ya kalasi, iye potsirizira pake akundipatsa bukhu lonena za mmene mungatsogozere kalankhulidwe ka m’kalasi molondola!”

Talingalirani kukhala wokhoza kuimirira kutsogolo kwa gulu ndi kuphunzitsa Baibulo—mwaluso, mofikapo! Iri liri kokha limodzi la mapindu omwe angadze kwa inu ngati mupezeka pa misonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu. Wonjezerani ku chimenecho kuyanjana kwabwino komwe mudzasangalala nako kumeneko, ndipo mungawone bwino lomwe mmene kupezeka mokhazikika ku misonkhano kuliri kofunika kukudyetsa chikhulupiriro chanu mwa Mulungu ndi Mwana wake. “Iye amene akhulupirira,” Yesu anakumbutsa tero, “alinawo moyo wosatha.”—Yohane 3:36.

Tikuyembekeza, chotero, kuti kukambitsirana kwachidule kumeneku kwadzutsa chilakolako chanu cha kuyamba kupezeka ku misonkhano ngati simunayambe kuchita tero. Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati inu mukupezeka kale? Chotero funso liri lakuti, Kodi mukutenga zochulukira pa misonkhano imeneyi monga mmene mufunikira? Kope la mtsogolo lidzakambitsirana chimenechi.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 22]

Misonkhano pa Nyumba ya Ufumu imapereka mwaŵi kaamba ka anthu achichepere kugawanamo mokangalika

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena