Lingaliro Labaibulo
Kodi Chipangano Chakale Chiri Chachikale?
◼ “Chipangano Chakale chimaphunzitsa udani ndi kubwezera, ‘diso pa diso ndi dzino pa dzino.’ Zonsezo zalowedwa m’malo ndi Chipangano Chatsopano, chomwe chimaphunzitsa chikondi ndi kukhululukira.”
◼ “Chipangano Chakale chiri kokha chosayenera kwa Akristu amakono, chotero sichiri choyenera nkomwe kuchiŵerenga icho!”
KODI munadzipezapo kale inu eni mukubwezera kulankhula komwe kuli pamwambapo, kapena kodi munamva winawake akuchita tero? Kodi Chipangano Chakale (Malemba Achihebri) m’chenicheni chiri chakufa, chachikale, cholowedwa m’malo ndi Chipangano Chatsopano (Malemba Achikristu Achigriki)? Kodi nchiyani chimene Baibulo ilo leni limanena?
Mosangalatsa, Chipangano Chatsopano chimasonyeza kuti Lamulo la chipangano, pangano limene Mulungu anapanga ndi Israyeli wakale, linatha ndipo chotero silikugwira ntchito pa Akristu. (Aefeso 2:15; Ahebri 8:13) Lamulo la pangano limeneli n’lophatikizidwa mu Chipangano Chakale. Koma kuli zochulukira zambiri ku Chipangano Chakale kuposa Lamulo la pangano!
Pali mbali zitatu za Chipangano Chakale zimene zimachipanga icho kukhala chofunika kwa inu. Kodi izo nchiyani? (1) Mbiri yofunika, (2) ndakatulo yomangilira, ndi (3) ulosi wodzetsa chikhulupiriro, zonse za mtengo wokulira kwa Akristu amakono. Lingalirani mmene ichi chiriri tero.
Mbiri ya Baibulo
Mabukhu oyambirira 17 a Chipangano Chakale, Genesis mpaka Estere, amagwirizanitsa zolembedwa za mbiri za zochita za Mulungu ndi munthu kuchokera ku chilengedwe chake mpaka zana lachisanu B.C.E. Koma ichi sichiri kokha mbiri yakufa! Monga mmene mtumwi Wachikristu Paulo analembera: “Koma izi [zolongosoledwa mu Chipangano Chakale] zinachitika zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowa analakalaka.”—1 Akorinto 10:11.
Nchifukwa ninji Paulo anawona mbiri imeneyi kukhala yofunika kaamba ka Akristu mosasamala kanthu za kupita kwa zaka mazana? Mwachidule chifukwa chakuti monga mmene chibadwa cha munthu sichinasinthire kwa zaka zonsezi moteronso Mulungu iyemwini sanasithe. (Malaki 3:6) Mtumwi Wachikristu Yakobo anati ponena za Yehova Mulungu: “Amene alibe chisanduliko kapena mthunzi wa chitembenukiro.” (Yakobo 1:17) Mthunzi wobweretsedwa ndi dzuŵa umasinthasintha kuchokera ku waung’ono masana kufikira utatambasulidwa polowa dzuŵa. Koma Yehova ali wosiyana; umunthu wake uli wosasintha.
Chotero, tingaphunzire zochulukira kuchokera ku mbiri ya zochita za Yehova ndi makolo akale, ndi Israyeli pa Nyanja Yofiira ndi m’chipululu, ndi anthu ena ambiri. Mwachitsanzo, monga mmene Mulungu analakwiridwa pamene Aisrayeli analambira mafano kapena kuchita dama choteronso iye samakondweretsedwa pamene Akristu adziloŵetsa m’kachitidwe koteroko. (1 Akorinto 10:1-12) Ngakhale Lamulo la pangano, ngakhale kuti silimagwira ntchito kwa Akristu, limapereka chidziŵitso chopindulitsa mu umunthu wa Yehova kupyolera m’maprinsipulo ake amaziko.
Ndakatulo ya Baibulo ndi Ulosi
Mabukhu asanu otsatira, kuchokera pa Yobu mpaka Nyimbo ya Solomo, ali mabukhu a ndakatulo. Koma mabukhu amenewa ali oposa kokha mabukhu abwino, popeza kuti zamkati mwawo ziri zolimbikitsa mwauzimu, ndipo kaŵirikaŵiri zozikidwa pa zochitika za m’mbiri. Kodi ndi malingaliro a yani omwe sanadzutsidwe ndi Masalmo? Ndipo ndani yemwe sangawone uphungu wogwira ntchito pa kuwona mtima, nsanje, ndi nkhani zina za maunansi a munthu m’bukhu la Miyambo? (Miyambo 11:1; 14:30) Mosakaikira, mabukhu amenewa ali opindulitsa lerolino monga mmene analiri pamene analembedwa poyambirira.
Mabukhu otsirizira 17 a Chipangano Chakale, Yesaya mpaka Malaki, ali mabukhu a ulosi. Iwo ali ndi kulengeza kwa aneneri akale Achihebri ndipo amapereka kulongosola kotheratu kwa kudza kwa pa dziko lapansi kwa Mesiya mazana ochuluka pasadakhale. Zolembedwa za Uthenga Wabwino mu Chipangano Chatsopano zimasonyeza kukwaniritsidwa kwa unyinji wa maulosi amenewo, ngakhale mu tsatanetsatane wa kalikonse kolowetsedwamo. Motsimikizirika, kulingalira kulongosoka kwa maulosi amenewa kumalimbikitsa chikhulupiriro chathu mwa Yesu Kristu monga mmodzi yemwe anatumizidwa ndi Mulungu kudzapulumutsa mtundu wa anthu!
Lodzitsutsa?
Koma kodi kusiyana pakati pa Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano kungagwirizanitsidwe? Tiyeni tichitire chitsanzo: Atate angalange ana ake achimuna aŵiri mosiyana chifukwa chakuti mwana aliyense ali ndi maumunthu osiyana. Mofananamo, kumvekera kwa uphungu wa Yehova m’Chipangano Chakale kwa Israyeli, mtundu wa anthu odzipereka kwa iye mwachibadwa, kukasiyana kuchokera ku kamvekedwe ka uphungu wopezeka mu Chipangano Chatsopano kwa mpingo Wachikristu, gulu la anthu odzipereka kwa iye mwa kusankha.
Chotero, kusanthula kosamalitsa kwa Baibulo kumasonyeza kuti mbali ziŵiri zimenezi siziri zotsutsana, koma, m’malomwake, zothandizana ina ndi inzake. Mbali zonsezo zimafunikira kaamba ka ‘munthu wa Mulungu kuti akhale woyenera, wofikapo kwenikweni.’—2 Timoteo 3:16, 17.
Mwachitsanzo, kodi Chipangano Chakale m’chenicheni chimalola kaamba ka kubwezera kwaumwini pamene kuli kwakuti Chipangano Chatsopano chimatsutsa ichi? Kutalitali! Zonse ziŵiri zimayamikira kukonda adani athu, zikumalozera kuti kubwezera kwasungidwa kaamba ka Mulungu. (Yerekezani Deuteronomo 32:35, 41 ndi Miyambo 25:21, 22 ku Aroma 12:17-21.) M’chenicheni, pamene Chipangano Chakale chilankhula za ‘diso pa diso ndi dzino pa dzino,’ sichikulankhula za kubwezera kwaumwini koma, m’malomwake, kubwezera koyenera monga momwe kunaikidwira ndi bwalo lamilandu loikidwa mwalamulo.—Eksodo 21:1, 22-25.
Ayi, Chipangano Chakale sichinathe ntchito kapena chotsutsa. Baibulo limatsimikizira kuti Chipangano Chakale chiri chamoyo ndipo chofunika kaamba ka Akristu lerolino monga mmene Chipangano Chatsopano chiriri. Kumbukirani mawu a Yesu Kristu: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse otuluka mkamwa mwa Mulungu.” Ndipo chimenecho chimaphatikiza osati kokha Malemba Achikristu Achigriki komanso Malemba Achihebri.—Mateyu 4:4; yerekezani ndi Deuteronomo 8:3.